LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • th phunzilo 14 tsa. 17
  • Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu
  • Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Zofanana
  • Muzibwelelamo mu Mfundo Zikulu-zikulu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Mawu Otsiliza Ogwila Mtima
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
th phunzilo 14 tsa. 17

PHUNZILO 14

Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu

Lemba losagwila mawu

Aheberi 8:1

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kukutsatilani m’nkhani yanu. Onetsani bwino mmene mfundo yaikulu iliyonse ikugwilizanila na colinga canu, komanso na mutu wa nkhani.

MOCITILA:

  • Khalani na colinga. Kodi colinga ca nkhani yanu ni kupeleka cidziŵitso, kukhutilitsa omvela anu pa nkhani inayake, kapena ni kuwalimbikitsa? Poikamba, onetsetsani kuti mfundo zazikulu zonse zikuthandizila kukwanilitsa colinga cimeneco.

    Tumalangizo tothandizila

    Dzifunseni kuti: ‘Kodi omvela anga angakhale na mafunso anji pa nkhani imeneyi? Nanga angakhalepo na maganizo osiyana ati? Kodi nikayankha funso lakuti-lakuti, ningautsenso mafunso ati m’maganizo mwawo?’ Sanjani mfundo zanu mwa dongosolo limenelo. Mukatelo, omvela anu adzakutsatilani mosavuta m’nkhani yanu, adzamvetsetsa, ndipo adzakhutila na mfundo zanu.

  • Gogomezani mutu wa nkhani. M’nkhani yanu yonse, muzikumbutsanso mutu wanu wa nkhani mwa kubweleza mawu ake ofunika kwambili, kapena kuchula mawu ena ofanana nawo tanthauzo.

  • Mfundo zanu zazikulu zizimveka bwino komanso mosavuta. Sankhani cabe mfundo zothandizila kumveketsa mutu wa nkhani, zimenenso mungazifotokoze bwino m’nthawi imene mwapatsidwa. Cepetsani mfundo zikulu-zikulu, fotokozani iliyonse payokha-payokha, ndipo cokani pa ina kupita pa inzake moonekela bwino.

    Tumalangizo tothandizila

    Mungachule mfundo zazikulu m’mawu anu oyamba kuti omvela anu athe kukutsatilani Kapena mungazibweleze m’mawu anu otsiliza pothandiza omvela anu kuti akazikumbukile.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani