LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 56
  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kuyandikila Abale ndi Alongo Athu n’Kwabwino Kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Musapunthwitse “Tianati”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tingatengele Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Yandikilani Banja Lanu Lauzimu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 56
Phunzilo 56. Alongo aŵili amafuko osiyana akupatsana moni mwansangala.

PHUNZILO 56

Sungani Mgwilizano wa Mpingo

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Tikakhala pakati pa olambila anzathu, timamva mmene Mfumu Davide anamvela. Iye anakamba kuti: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!” (Salimo 133:1) Umodzi wathu sumangocitika wokha. Aliyense wa ife amacita mbali yake kuti tiulimbikitse.

1. Kodi cimacititsa cidwi n’ciyani pakati pa anthu a Mulungu?

Ngati mungakapezeke pa msonkhano wa mpingo kudziko lina, mwina simungamve cinenelo ca kumeneko. Komabe mumakhala womasuka m’njila zambili. Cifukwa ciyani? Cifukwa kulikonse kumene tingakhale timaphunzila Baibo pogwilitsa nchito mabuku amodzimodzi. Ndiponso, timayesetsa kuonetsana cikondi wina na mnzake. Zilibe kanthu tikukhala kuti, tonse “timaitanila pa dzina la Yehova ndi kumutumikila mogwilizana.”—Zefaniya 3:9.

2. Kodi inuyo mungacite ciyani kuti mulimbikitse mgwilizano umenewo?

“Kondanani kwambili kucokela mumtima.” (1 Petulo 1:22) Kodi uphungu umeneyu mungauseŵenzetse bwanji? M’malo moyang’ana pa zofooka za ena, yang’anani pa makhalidwe awo abwino. M’malo mwakuti muzingoyanjana na aja amene mumakonda nawo zinthu zofanana, yesani kumacezanso na abale komanso alongo amene mumasiyana nawo m’njila zina. Tiyenelanso kuyesetsa ndithu kucotselatu maganizo a tsankho alionse amene tingakhale nawo. Ŵelengani 1 Petulo 2:17.a

3. Kodi muyenela kucita ciyani mukasemphana maganizo na Mkhristu mnzanu?

Ndife ogwilizana inde, koma sitili angwilo. Nthawi zina tingakhumudwitsane kapena kukwiyitsana wina na mnzake. Conco Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.” Ndipo amawonjezela kuti: “Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Ŵelengani Akolose 3:13) Ngakhale kuti Yehova takhala tikumukwiyitsa maulendo osaŵelengeka, iye amatikhululukilabe. Conco, iye amatiyembekezela kucita cimodzimodzi kwa abale athu. Mukazindikila kuti mwakwiyitsa munthu wina, khalani woyamba kucitapo kanthu kuti muyanjanenso.—Ŵelengani Mateyu 5:23, 24.b

KUMBANI MOZAMILAPO

Yesani kupeza njila zimene mungathandizile kusungitsa mgwilizano na mtendele mu mpingo.

Zithunzi: M’bale akusungitsa mtendele. 1. M’bale wina akulankhula kwa iye mwaukali. 2. Iye akuganizila zimene m’bale winayo wakamba. 3. Akuganizilanso zimene Baibo imatilangiza kucita munthu wina akatikhumudwitsa. 4. Iye wapempha m’baleyo kuti akamwe naye limodzi khofi, ndipo akubwezeletsa mtendele.

Kodi muyenela kucita ciyani kuti musungitse mtendele?

4. Pewani tsankho

Timafuna kukonda abale athu onse. Koma nthawi zina cingakhale cotivuta kukonda munthu amene timasiyana naye m’njila zina. Kodi zikatelo tiyenela kucita ciyani? Ŵelengani Machitidwe 10:34, 35, na kukambilana mafunso aya:

  • Yehova amalandila anthu a mtundu uliwonse kukhala Mboni zake. Kodi kudziŵa zimenezi kuyenela kutithandiza kumawaona motani anthu amene timasiyana nawo?

  • Kodi kwanuko kuli mitundu yotani ya tsankho imene muyenela kuipewa?

Ŵelengani 2 Akorinto 6:11-13, na kukambilana funso ili:

  • Kodi muyenela kucita ciyani kuti muzikonda abale na alongo a mitundu ina, kapena a zikhalidwe zina?

5. Muzikhululuka na mtima wonse komanso muzisungitsa mtendele

Yehova amatikhululukila na mtima wonse, ngakhale kuti iye sakafunikilapo kuti tikamukhululukile. Ŵelengani Salimo 86:5, na kambilanani mafunso aya:

  • Kodi cikhululukilo ca Yehova n’cacikulu motani?

  • N’cifukwa ciyani mumayamikila kuti Yehova amakhululuka?

  • N’zocitika ziti zingapangitse kuti tisamagwilizane bwino na anthu ena?

Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani ya kukhululuka kuti tikhalebe ogwilizana monga abale na alongo? Ŵelengani Miyambo 19:11, na kukambilana funso ili:

  • Ngati munthu wina wakukwiyitsani, kapena wakukhumudwitsani, kodi muyenela kucita ciyani kuti musungitse mtendele?

Nthawi zina timakhumudwitsa anthu ena. Zimenezi zikacitika, kodi tiyenela kucita bwanji? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila

VIDIYO: Kukhazikitsa Mtendele Kumabweletsa Madalitso (6:01)

  • Kodi mlongo wa mu vidiyo iyi anacita ciyani kuti asungitse mtendele?

6. Muziyang’ana pa zabwino mwa abale na alongo anu

Tikamagwilizana bwino na abale komanso alongo athu, m’pamene timadziŵa mbali zimene amacita bwino, na zofooka zawo. Koma tingacite bwanji kuti tiziyang’ana kwambili pa mbali zimene amacita bwino? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

VIDIYO: Khalani Munthu Wabwino Kwambili! (5:10)

  • Kodi cingakuthandizeni n’ciyani kuti muziona makhalidwe abwino mwa abale na alongo anu?

Yehova amayang’ana pa makhalidwe athu abwino. Ŵelengani 2 Mbiri 16:9a, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji podziŵa kuti Yehova amayang’ana pa mbali zimene mumacita bwino?

Ling’i ya daimondi.

Mwala wokongola wa daimondi umakhalabe na mbali zina zosakhala bwino. Ngakhale n’telo, umakhalabe mwala wa mtengo wapatali kwambili. N’cimodzi-modzinso abale na alongo athu. Onse ni opanda ungwilo inde, koma ni a mtengo wapatali kwa Yehova

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuti nikhululukile munthu, afunika kupepesa coyamba.”

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala na mtima wokhululuka?

CIDULE CAKE

Mungathandize kusunga mgwilizano mu mpingo ngati mukhala munthu wokhululuka, komanso mukamaonetsa cikondi kwa abale na alongo anu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi muyenela kucita ciyani kuti muzipewa tsankho?

  • Nanga muyenela kucita ciyani mukasemphana maganizo na Mkhristu mnzanu?

  • N’cifukwa ciyani muyenela kutengela citsanzo ca Yehova ca kukhululuka?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani mmene fanizo la Yesu lingatithandizile kuti tizipewa kuweluza ena.

Cotsani Mtanda wa Denga (6:56)

Kodi tiyenelabe kupepesa ngati tiona kuti sitinalakwitse ciliconse?

“Kupepesa—Njira Yothandiza Yopezera Mtendere” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2002)

Onani mmene amuna aŵili okulila m’dziko losankhana mitundu anapezela mgwilizano weniweni.

Johny na Gideon: Anali Adani, Tsopano ni Abale (6:42)

Onani zimene muyenela kucita kuti kusemphana maganizo kwanu kusawononge mtendele wa mpingo.

“Tizithetsa Mikangano Mwamtendele” (Nsanja ya Mlonda, May 2016)

a Mfundo ya kumapeto 6 imaonetsa kuti cikondi cimapangitsa Akhristu kupewa kuyambukiza ena matenda opatsilana.

b Mfundo ya kumapeto 7 iunikila mmene mungathetsele nkhani zamalonda komanso zokhudza malamulo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani