Mavuto Adzatha Posacedwapa!
Yelekezelani kuti mukukhala m’dziko lopanda zaupandu, nkhondo, matenda ndi masoka acilengedwe. Yelekezelani kuti m’mawa uliwonse mukudzuka mulibe nkhawa ndi mavuto a zacuma, tsankho kapena kupondelezana. Kodi inu muona kuti zimenezi n’zosatheka? N’zoona kuti palibe munthu kapena bungwe la anthu limene lingathetse mavuto amenewa. Koma Mulungu walonjeza kuti adzacotsa zinthu zonse zimene zimapangitsa mavuto a anthu, kuphatikizapo zimene tinakambilana m’nkhani yapita. Onani zinthu izi zimene Mulungu walonjeza m’Mau ake, Baibo:
◼ PADZAKHALA BOMA LABWINO
“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzaonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kale-kale.”—Danieli 2:44.
Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Wolamulila wake osankhidwa, Yesu Kristu, adzalamulila m’malo mwa ulamulilo wa anthu, ndipo iye adzapangitsa kuti cifunilo ca Mulungu cicitike kumwamba ndi padziko lapansi pano. (Mateyu 6:9, 10) Boma limeneli silidzaloŵedwa m’malo ndi boma lililonse la anthu cifukwa cakuti ilo ndi “ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu.” Zimenezi zidzabweletsa mtendele wosatha.—2 Petulo 1:11.
◼ CIPEMBEDZO CONAMA CIDZAONONGEDWA
“Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala. Conco n’zosadabwitsa ngati atumiki ake naonso amadzisandutsa atumiki a cilungamo. Koma mapeto ao adzakhala monga mwa nchito zao.”—2 Akorinto 11:14, 15.
Cipembedzo conama cidzadziŵika kuti ndi nchito za Mdyelekezi ndipo cidzaonongedwa kothelatu. Tsankho ndi kuphana kwa cipembedzo zidzatha. Zimenezi zidzacititsa kuti anthu onse okonda “Mulungu wamoyo ndi woona” am’tumikile ndi “cikhulupililo cimodzi” ndiponso “motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” Izi zidzabweletsa mtendele ndi mgwilizano.—1 Atesalonika 1:9; Aefeso 4:5; Yohane 4:23.
◼ ANTHU ADZAKHALA ANGWILO
“Mulunguyo adzakhala nao. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Yehova Mulungu adzacita zimenezi kupyolela mwa Mwana wake, Yesu, amene anapeleka moyo wake kaamba ka anthu. (Yohane 3:16) Mu ulamulilo wa Yesu, anthu adzakhala angwilo. Sikudzakhala mavuto cifukwa cakuti “Mulunguyo adzakhala nao” ndipo “adzapukuta misozi yonse m’maso mwao.” Posacedwapa, kupanda ungwilo kwa anthu ndi mavuto zidzacoka. “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
◼ MIZIMU YOIPA IDZACOTSEDWA
“[Yesu Kristu] anagwila cinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyelekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000. Ndipo anamuponyela m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo cidindo kuti asasoceletsenso mitundu ya anthu.”—Chivumbulutso 20:2, 3.
Ulamulilo wa Satana udzatha pamene iye ndi ziwanda adzamangidwa ndi kuponyedwa m’phompho” ndipo sadzakwanitsa kucita ciliconse. Ulamulilo wao woipa pa anthu udzatha. Panthawiyo tidzapeza mpumulo waukulu cifukwa cokhala m’dziko lopanda cisonkhezelo coipa ca Satana ndi ziwanda.
◼ “MASIKU OTSILIZA” ADZATHA
“Masiku otsiliza” adzatha kumapeto kwa “cisautso cacikulu” cimene Yesu anakamba. Iye anati: “Pa nthawiyo kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano, ndipo sicidzacitikanso.”—Mateyu 24:21.
Cisautso cimeneco cidzakhala cacikulu cifukwa cakuti padzakhala mavuto oopsa amene sanacitikepo m’mbuyomu. Mavuto amenewo adzakula kwambili pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ imene imachedwa “Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16.
Anthu onse amene amacita zabwino akuyembekezela mwacidwi kutha kwa dongosolo loipali la zinthu. Onani ena mwa madalitso amene io adzalandila mu Ufumu wa Mulungu.
MULUNGU ADZACITA ZOPOSA PAMENEPA
“Khamu lalikulu la anthu” lidzapulumuka ndi kuloŵa m’dziko latsopano la mtendele: Mau a Mulungu amanena kuti “khamu lalikulu la anthu” osaŵelengeka ‘lidzatuluka m’cisautso cacikulu’ ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14; 2 Petulo 3:13) Iwo adzakamba kuti cipulumutso cao cacokela kwa Yesu Kristu, “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akucotsa ucimo wa dziko.”—Yohane 1:29.
Anthu adzapindula kwambili cifukwa cophunzitsidwa ndi Mulungu: M’dziko latsopano, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova.” (Yesaya 11:9) Maphunzilo ocokela kwa Mulungu amenewo adzaphatikizapo malangizo okhudza mmene anthu onse angakhalile pamodzi mwamtendele popanda kuononga cilengedwe. Mulungu walonjeza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.”—Yesaya 48:17.
Okondedwa athu amene anafa adzauka: Pamene Yesu anali padziko lapansi anaukitsa bwenzi lake Lazaro amene anali atafa. (Yohane 11: 1, 5, 38-44) Motelo, iye anaonetsa kuti mu Ufumu wa Mulungu adzacita zazikulu kuposa pamenepa.—Yohane 5:28, 29.
Mtendele ndi cilungamo sizidzatha: Mu ulamulilo wa Kristu, simudzakhala anthu ophwanya malamulo. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi? Tidziŵa zimenezi cifukwa Yesu amakwanitsa kudziŵa za mumtima, ndipo adzagwilitsila nchito nzelu zake kuweluza olungama ndi oipa. Anthu amene safuna kusiya makhalidwe ao oipa sadzakhala m’dziko latsopano la Mulungu.—Salimo 37:9, 10; Yesaya 11:3, 4; 65:20; Mateyu 9:4.
Takambilana maulosi ocepa cabe a m’Baibo amene amafotokoza zinthu zosangalatsa zimene zidzacitika mtsogolo. Pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lapansi, kudzakhala “mtendele woculuka” umene sudzatha. (Salimo 37:11, 29) Zinthu zonse zimene zimapangitsa kuti anthu azivutika zidzacotsedwa. Timakhulupilila zimenezi cifukwa cakuti Mulungu walonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano. . . . Mau awa ndi odalilika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:5.
[Eni ake]
© Silke Woweries/Corbis