NKHANI YA PACIKUTO: KODI BAIBO IMAKAMBA—ZA CIANI?
N’cifukwa Ciani Mufunikila Kucita Cidwi ndi Baibo?
Baibo ndi buku lofala kwambili kuposa buku lililonse padziko lapansi. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti ndi yosavuta kuimvetsetsa. Imafotokoza nkhani zokhudza anthu eni-eni, mmene io anali kukhalila ndi anzao ndiponso ubwenzi wao ndi Mulungu. Nkhani zimenezi zimatiphunzitsa mfundo zothandiza mwa kugwilitsila nchito mau osavuta kumva ndi olunjika. Ndiponso zingatembenuzidwe m’zinenelo zambili cakuti anthu padziko lonse angazimvetsetse mosavuta. Ndipo mfundo za m’Baibo n’zothandiza nthawi zonse.
Koposa zonse, Baibo ndi buku limene limafotokoza za Mulungu, ndipo linacokela kwa Mulungu. Imatiuza dzina la Mulungu, makhalidwe ake ndi colinga cimene analengela dziko lapansi ndi anthu. Baibo imafotokoza mmene Satana anatsutsila ulamulilo wabwino wa Yehova, mmene Yehova adzaonetsela kuti Satana ndi wabodza ndiponso mmene Iye adzathetsela kuipa konse. Kuŵelenga Baibo ndi mtima wofuna kudziŵa zambili kungatithandize kukhala ndi cikhulupililo ndi ciyembekezo.
Baibo imafotokoza zinthu zimene sitingaphunzile kwina kulikonse. Mwacitsanzo, Baibo imatiuza coonadi pankhani monga izi:
▪ Kumene tinacokela ndiponso cifukwa cake timavutika
▪ Zimene Mulungu wakonza kuti apulumutse anthu
▪ Zimene Yesu anaticitila
▪ Zimene zidzacitikila dziko ndi anthu mtsogolo
Bwanji osapatula nthawi kuti muŵelenga masamba otsatila kuti muidziŵe bwino Baibo?
[Bokosi papeji 3]
DZIŴANI IZI PONENA ZA BAIBO
Nkhani yake yaikulu: Mmene Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzabweletsela cilungamo ndi mtendele padziko lapansi
Za mkati: Ili ndi mabuku 39 olembedwa m’Ciheberi (mbali zina zocepa zinalembedwa m’Ciaramu) ndipo ena 27 analembedwa m’Cigiriki
Kulembedwa kwake: Inalembedwa ndi amuna 40 kwa zaka zoposa 1,600, kucokela mu 1513 B.C.E. mpaka ca ku ma 98 C.E.
Zinenelo: Baibo yonse kapena mbali yake, yatembenuzidwa m’zinenelo zoposa 2,500