LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 masa. 9-13
  • Cilengedwe Cimadziŵikitsa Mulungu Wamoyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cilengedwe Cimadziŵikitsa Mulungu Wamoyo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIKHULUPILILO CIMAZIKIDWA PA UMBONI NDI MFUNDO ZOMVEKA
  • CILENGEDWE CIMAONETSA MPHAMVU ZA MULUNGU
  • CILENGEDWE CIMAONETSA NZELU ZA MULUNGU
  • THANDIZANI ENA KULEMEKEZA MULUNGU WAMOYO
  • Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Mumayamikila Mphatso Zimene Mulungu Anakupatsani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Limbitsani Cikhulupililo Canu mwa Mlengi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Gwilitsani Nchito Zacilengedwe Pophunzitsa Ana Anu za Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 10/1 masa. 9-13

Cilengedwe Cimadziŵikitsa Mulungu Wamoyo

“Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu . . . kulandila ulemelelo . . . cifukwa munalenga zinthu zonse.”—CHIV. 4:11.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi tiyenela kucita ciani kuti tigwetse ziphunzitso zabodza “zozikika molimba”?

Kodi cilengedwe cimaonetsa bwanji mphamvu ndi nzelu za Mulungu?

Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kulimbitsa cikhulupililo cao mwa Yehova?

1. Kodi tiyenela kucita ciani kuti cikhulupililo cathu cikhalebe colimba?

ANTHU ambili amakamba kuti akaona zinthu m’pamene amakhulupilila zinthu zimenezo. Kodi anthu otelo tingawathandize bwanji kukhulupilila Yehova? Baibo imakamba kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yoh. 1:18) Conco, kodi tingacite bwanji kuti cikhulupililo cathu mwa “Mulungu wosaonekayo,” Yehova, cikhalebe colimba? (Akol. 1:15) Njila yoyamba ndi kudziŵa ziphunzitso zimene zingatilepheletse kudziŵa coonadi ponena za Yehova. Ndiyeno tiyenela kugwilitsila nchito Baibo mwaluso kuti tigubuduze maganizo ‘otsutsana ndi kudziŵa Mulungu.’—2 Akor. 10:4, 5.

2, 3. Kodi ndi ziphunzitso ziŵili ziti zimene zimacititsa kuti anthu asadziŵe coonadi ponena za Mulungu?

2 Ciphunzitso cimodzi cabodza cimene cimalepheletsa anthu kudziŵa coonadi ponena za Mulungu ndi ciphunzitso ca cisanduliko. Ciphunzitso ca anthu cimeneci cimatsutsana ndi Baibo ndipo cimapangitsa kuti anthu asakhale ndi ciyembekezo. Ciphunzitso ca cisanduliko cimanena kuti moyo unangokhalako wokha. Conco, okhulupilila cisanduliko amaona kuti moyo wa munthu ulibe phindu.

3 Anthu ena a m’Machalichi Acikristu amaphunzitsa kuti cilengedwe conse kuphatikizapo dziko lapansi ndi za moyo zonse, zinalengedwa zaka masauzande ocepa zapitazo. Anthu amene amaphunzitsa zimenezi angakhale kuti amalemekeza Baibo, koma io amakhulupilila kuti zaka masauzande ocepa zapitazo Mulungu analenga zinthu zonse kwa masiku 6, tsiku lililonse lokhala ndi maola 24. Iwo amakana umboni woona wa sayansi umene umaonetsa kuti ciphunzitso cao n’cabodza. Conco, ciphunzitso cimeneci cimapeputsa Baibo, kuionetsa monga ndi yabodza. Anthu amene amacilikiza maganizo amenewa ali ngati anthu ena a m’nthawi za atumwi amene anali odzipeleka potumikila Mulungu ‘koma sanali kumudziŵa molondola.’ (Aroma 10:2) Kodi tingagwilitsile nchito bwanji Mau a Mulungu kuti ‘tigwetse ziphunzitso zozikika molimba’ za cisanduliko ndi ziphunzitso zina zabodza?a Tingacite zimenezi kokha ngati timaphunzila mwakhama kuti tipeze cidziŵitso colondola ca m’Baibo.

CIKHULUPILILO CIMAZIKIDWA PA UMBONI NDI MFUNDO ZOMVEKA

4. Kodi cikhulupililo cathu ciyenela kukhala cozikidwa pa ciani?

4 Baibo imatiuza kuti tiyenela kupitilizabe kuphunzila zinthu zamtengo wapatali. (Miy. 10:14) Yehova amafuna kuti cikhulupililo cathu mwa iye cikhale cozikidwa pa umboni ndi mfundo zomveka, osati pa nzelu za anthu kapena miyambo ya cipembedzo. (Ŵelengani Aheberi. 11:1) Kuti tikhale ndi cikhulupililo colimba mwa Mulungu, coyamba tiyenela kukhala otsimikiza kuti Yehova aliko. (Ŵelengani Aheberi 11:6.) Timakhulupilila zimenezi cifukwa copenda umboni woonetsa kuti iye aliko ndi kugwilitsila nchito ‘luntha lathu la kuganiza.’—Aroma 12:1.

5. N’cifukwa cimodzi citi cimene tingakhulupilile kuti Mulungu aliko?

5 Mtumwi Paulo anapeleka cifukwa cimodzi cokhulupilila kuti Mulungu aliko, ngakhale kuti sitingamuone. Ponena za Yehova, iye analemba kuti: “Cilengedwele dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Kodi munthu amene amakaikila kuti Mulungu aliko mungam’thandize bwanji kuona kuti mau ouzilidwa a Paulo amenewa ndi oona? Mungakambitsilane naye maumboni ena otsatilawa a zacilengedwe amene amaonetsa mphamvu ndi nzelu za Mlengi wathu.

CILENGEDWE CIMAONETSA MPHAMVU ZA MULUNGU

6, 7. Kodi zinthu ziŵili zimene zimatiteteza zimaonetsa bwanji mphamvu za Yehova?

6 Mphamvu za Yehova zimaonekela m’zinthu ziŵili zimene zimatiteteza. Zinthu zimenezi ndi mlenga-lenga ndi mphamvu yokoka ya dziko. Mwacitsanzo, mu mlenga-lenga muli zinthu zambili osati cabe mpweya umene timapuma. Mulinso mpweya umene umatiteteza ku zinthu zimene zimayenda-yenda m’mwamba. Miyala yoyenda-yenda m’mwamba imene ingaononge dziko imapsa ikafika mu mlenga-lenga, ndipo imaoneka ngati nyenyezi zothamanga m’mwamba usiku.

7 Mphamvu yokoka ya dziko nayonso imatiteteza ku zinthu zimene zingativulaze. Mphamvu imeneyi imacokela pansi padziko. Pansi padziko pali mwala wacitsulo wotentha kwambili umene umatulutsa mphamvu yokoka ya dziko imene ili paliponse padziko lapansi, ndipo imafika m’mwamba kwambili. Mphamvu imeneyi imatiteteza kuti kutentha kovulaza kwa dzuŵa kusafike padziko lapansi. Kutentha kumeneku kumathetsedwa ndi mphamvu imeneyo kuti zamoyo padziko zisaonongeke. Umboni wakuti mphamvu yokoka imeneyi ilipo ndi kuwala kokongola kumene kumaoneka m’mwamba kumpoto ndi kumwela kwa dziko. Ndithudi, Yehova “ali ndi mphamvu zambili zocitila zinthu.”—Ŵelengani Yesaya 40:26.

CILENGEDWE CIMAONETSA NZELU ZA MULUNGU

8, 9. Kodi kayendedwe ka zinthu zimene zimacilikiza moyo kamaonetsa bwanji nzelu za Yehova?

8 Zimene Yehova wacita kuti padziko pakhalebe zamoyo zimaonetsa nzelu zake. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti mukukhala mumzinda umene uli ndi mpanda ndipo uli ndi anthu ambili. Mumzindawo mulibe njila yobweletsela madzi abwino kucokela kunja ndi kutulutsa zinthu zonyansa. Posakhalitsa mzinda umenewo ungakhale wauve ndipo anthu sangakonde kukhalamo. Dziko lathu lili ngati mzinda wotelo. Padziko lapansi pali madzi okwanila koma sitingathe kucotsa zinthu zonyansa zonse padzikoli. Komabe, dzikoli lakwanitsa kucilikiza zamoyo mabiliyoni ambili kwa zaka zambili-mbili. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti limakwanitsa kukonza ndi kugwilitsilanso nchito zinthu zocilikiza moyo zimene zili padzikoli.

9 Ganizilani kayendedwe ka mpweya wa oxygen. Zamoyo mabiliyoni ambili zimagwilitsila nchito mpweya wabwino wa oxygen ndipo zimatulutsa mpweya woipa wa carbon dioxide. Ngakhale zili conco, mpweya wa oxygen sumatha ndipo mu mlenga-lenga simudzala mpweya woipa wa carbon dioxide. N’cifukwa ciani zili conco? Cimene cimacititsa zimenezi ndi njila yodabwitsa imene zomela zimapangila zakudya. Popanga zakudya, zomela zobiliŵila zimagwilitsila nchito mpweya wa carbon dioxide, madzi, kuwala kwa dzuŵa ndi zinthu zina za m’nthaka. Panthawi imodzi-modziyo zimatulutsa mpweya wa oxygen. Nthawi zonse, ifeyo timapuma mpweya wa oxygen umenewu ndi kutulutsa mpweya wa carbon dioxide. Izi zimathandiza kuti zomela nazonso zipeze mpweya wopangila cakudya. Conco, tinganene kuti Yehova amagwilitsila nchito zomela zimene anapanga kuti apatse ‘anthu onse moyo ndi mpweya.’ (Mac. 17:25) Zimenezi zimaonetsa nzelu zodabwitsa za Mulungu.

10, 11. Kodi gulugufe ndi bembelezi zimaonetsa bwanji nzelu za Yehova?

10 Timaonanso nzelu za Yehova tikaganizila mmene iye anapangila zamoyo zambili-mbili zimene zili padziko lapansi. Anthu ofufuza amanena kuti mitundu ya zamoyo padziko lapansi ilipo pakati pa 2 miliyoni mpaka 100 miliyoni. (Ŵelengani Salimo 104:24.) Onani mmene zina mwa zamoyo zimenezi zimaonetsela nzelu za Mulungu.

11 Mwacitsanzo, gulugufe wina wamkulu wa ku America ali ndi ubongo waung’ono ngati nsonga ya bopeni. Koma gulugufe ameneyo amakwanitsa kuyenda mtunda wa makilomita pafupi-fupi 3,000, kucokela ku Canada kupita ku nkhalango ina ya ku Mexico motsatila kayendedwe ka dzuŵa. Kodi gulugufe ameneyo amakwanitsa bwanji kuyenda dzuŵa likacoka kumbali ina kupita kumbali ina? Yehova anapanga ubongo wa gulugufe ameneyo kuti azitha kudziŵa njila yoyenela kuyenda ngakhale pamene dzuŵa lapita kumbali ina. Ndiponso ganizilani bembelezi kapena kuti nanjelezi. Iye ali ndi maso aŵili aakulu. Diso lililonse lili ndi tuzigawo pafupi-fupi 30,000 tumene tumathandiza bembelezi kuona. Ngakhale zili conco, iye amakwanitsa kuzindikila zinthu zambili zimene amaona ndi maso ake. Amazindikila ngakhale kugwedezeka kocepa kwambili kwa zinthu zimene zili pafupi naye.

12, 13. N’ciani cimakucititsani cidwi ndi mmene Yehova anapangila maselo a thupi lathu?

12 Cinthu cocititsa cidwi kwambili ndi mmene Yehova anapangila maselo a zamoyo zonse. Mwacitsanzo, thupi lathu linapangidwa ndi maselo pafupi-fupi 100 thililiyoni. Mkati mwa selo lililonse muli kanthu kokhala ngati kanthambo kochedwa DNA (deoxyribonucleic acid). DNA imasunga malangizo ofunika popanga thupi la munthu.

13 Kodi DNA imasunga malangizo oculuka bwanji? Tingayelekezele kuculuka kwa malangizo amene galamu imodzi ya DNA imasunga ndi zinthu zimene CD imasunga. CD ingasunge zinthu zonse zolembedwa mu dikishonale ndipo izi ndi zocititsa cidwi cifukwa cakuti CD ndi kanthu kakang’ono kwambili. Koma galamu imodzi cabe ya DNA ingasunge malangizo okwanila ma CD 1 thililiyoni. M’mau ena tinganene kuti DNA yodzala sipuni imodzi yaing’ono ingasunge malangizo okwanila kupanga anthu pafupi-fupi 2.5 thililiyoni.

14. Kodi zimene asayansi anatulukila zapangitsa kuti muzimuona bwanji Yehova?

14 Mfumu Davide inafotokoza kuti malangizo opangila thupi la munthu amakhala ngati kuti analembedwa m’buku lophiphilitsa. Ponena za Yehova Mulungu, iye anati: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale ciwalo cimodzi cimene cinali citapangidwa.” (Sal. 139:16) N’zosadabwitsa kuti pamene Davide anaganizila mmene thupi lake linapangidwila, anatamanda Yehova. Zimene asayansi anatulukila zaka zapitazi zapangitsa kuti tiziopa kwambili Yehova tikaganizila mmene iye anatipangila. Kaamba ka zimenezi, timagwilizana ndi zimene wamasalimo analemba ponena za Yehova kuti: “Ndidzakutamandani cifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandicititsa mantha. Nchito zanu ndi zodabwitsa, ndipo ine ndimadziŵa bwino zimenezi.” (Sal. 139:14) Ndithudi, cilengedwe cimatitsimikizila kuti Mulungu alikodi.

THANDIZANI ENA KULEMEKEZA MULUNGU WAMOYO

15, 16. (a) Kodi zofalitsa zathu zatilimbikitsa bwanji kuyamikila mphamvu za Yehova za kulenga? (b) Kodi ndi nkhani iti ya mutu wakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” imene inakusangalatsani kwambili?

15 Kwa zaka zambili, magazini ya Galamukani! yathandiza anthu mamiliyoni ambili kuzindikila kuti cilengedwe cimaonetsa kuti kuli Mulungu wamoyo. Mwacitsanzo, mu Galamukani! ya September 2006 munali nkhani yakuti “Kodi Mlengi Alipo?” Colinga ca magazini iyi cinali kuthandiza anthu amene acititsidwa khungu ndi ciphunzitso ca cisanduliko ndi ziphunzitso zina zabodza. Ponena za magazini imeneyi, mlongo wina analembela kalata ofesi ya nthambi ya ku United States. Iye anati: “Nchito yogaŵila magazini yapadela imeneyi inayenda bwino kwambili. Mai wina anapempha magazini 20. Iye ndi mphunzitsi wa sayansi yokhudza zinthu zamoyo ndipo anafuna kuti ana a m’kalasi lake akhale ndi magazini ao.” M’bale wina analemba kuti: “Ine ndakhala ndikulalikila mwakhama kuyambila kumapeto kwa zaka za m’ma 1940, ndipo panthawi ino ndili ndi zaka pafupi-fupi 75. Koma sindinasangalalepo ndi ulaliki monga mmene ndacitila mwezi uno pamene ndinali kugaŵila magazini yapadela ya Galamukani! imeneyi.”

16 Kuyambila zaka zaposacedwapa, m’magazini ambili a Galamukani! mumapezeka nkhani yakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” Nkhani zimenezi zimaonetsa mmene zolengedwa zinapangidwila mwaluso ndiponso zimafotokoza zimene anthu acita poyesa kukopela zimene Wolinganiza Wamkulu anacita. Mu 2010, kunatuluka kabuku kacingelezi kakuti Was Life Created? kamene kamatithandiza kulemekeza Mulungu. Zithunzi-thunzi zokongola ndi zinthu zina zimene zili mu kabuku kameneka, colinga cake ndi kutilimbikitsa kuyamikila mphamvu za Yehova za kulenga. Mafunso amene ali kumapeto kwa cigawo ciliconse amathandiza munthu kuganizila zimene waŵelenga. Kodi mumakonda kugwilitsila nchito kabuku kameneka polalikila?

17, 18. (a) Makolo, kodi mungathandize bwanji ana anu kukhala okonzeka kuteteza cikhulupililo cao? (b) Kodi mwatugwilitsila nchito motani tumabuku tonena za cilengedwe pa kulambila kwanu kwa pabanja?

17 Inu makolo, kodi munagwilitsilako nchito kabuku kokongola aka pa kulambila kwa pabanja ndi ana anu? Mukacita zimenezi, mudzawathandiza kuyamikila Mulungu wathu wamoyo. Mwina muli ndi ana acinyamata amene amaphunzila kusukulu ya sekondale. Kaŵili-kaŵili io amakumana ndi anthu amene amaphunzitsa ciphunzitso cabodza ca cisanduliko. Asayansi ndi aphunzitsi amalimbikila kukamba kuti ciphunzitso cisanduliko ndi coona. Komanso mapulogilamu ofotokoza za cilengedwe ndi zosangulutsa monga mafilimu zimalimbikitsa mfundo imeneyi. Mungathandizenso ana anu kulimbana ndi mfundo zabodza zimenezi mwa kugwilitsila nchito kabuku kena kacingelezi kakuti, The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, kamene kanatulutsidwa mu 2010. Mofanana ndi kabuku kakuti Was Life Created?, kabuku aka kamalimbikitsa acinyamata kukhala ‘oganiza bwino.’ (Miy. 2:10, 11) Kamawaphunzitsa mmene angadziŵile ngati zimene amaphunzila kusukulu pankhaniyi ndi zoona kapena ai.

18 Kabuku kakuti Origin of Life kanapangidwa kuti kathandize ana a sukulu kupenda nkhani zonama zakuti asayansi anapeza zinthu za m’matongwe zoonetsa kuti ciphunzitso ca cisanduliko ndi coona. Kamawalimbikitsa kupenda nkhani zimenezo kuti aone ngati zimatsimikiziladi kuti munthu anacokela ku nyama. Ndiponso kamawaphunzitsa mmene angayankhile zokamba za anthu zakuti asayansi apeleka umboni wokwanila wakuti moyo ungakhalepo wokha. Makolo, ngati mugwilitsila nchito tumabuku tumenetu, mungathandize ana anu kukhala okonzeka kuyankha anthu amene amawafunsa cifukwa cake amakhulupilila kuti kuli Mlengi.—Ŵelengani 1 Petulo 3:15.

19. Kodi tonsefe tili ndi mwai wotani?

19 Tingaphunzile zambili za makhalidwe apamwamba a Yehova tikamaŵelenga nkhani za cilengedwe m’mabuku amene timalandila m’gulu la Yehova. Umboni wa m’mabuku awa umatilimbikitsa kutamanda kwambili Mulungu wathu. (Sal. 19:1, 2) Tili ndi mwai waukulu kwambili wopeleka ulemu ndi ulemelelo kwa Yehova umene iye amayenelela monga Mlengi wa zinthu zonse.—1 Tim. 1:17.

[Footnote]

a Kuti mudziŵe zimene mungakambe kwa munthu amene amakhulupilila kuti zinthu zonse zinalengedwa zaka masauzande ocepa zapitazo, onani kabuku kacingelezi kakuti Was Life Created? tsamba 24 mpaka 28.

[Zithunzi papeji 11]

Kapangidwe ka diso la bembelezi (nanjelezi) kamaonetsa nzelu za Mulungu; diso lake akalikulitsa (Onani ndime 11)

[Eni ake]

Cithunzi-thunzi ca diso: Boris Krylov, www.macro-photo.org

[Zithunzi papeji 13]

Makolo, konzekeletsani ana anu kuteteza cikhulupililo cao (Onani ndime 17)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani