NKHANI YA PACIKUTO
Kodi Ndani Amadziŵadi Zamtsogolo?
Tonsefe timaganizila za mtsogolo. Timafunitsitsa kudziŵa mmene umoyo wathu kapena wa okondedwa athu udzakhalila. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ana anga adzakhala ndi tsogolo labwino? Kodi dziko lidzaonongedwa ndi ngozi zacilengedwe? Ndingasinthe ciani kuti ndikhale ndi tsogolo labwino?’ Mwacibadwa, timafuna kutsimikizila umboni wa zinthu ndi kudziŵa ngati zinthuzo zidzacitikadi. Kudziŵa bwino zamtsogolo kudzakuthandizani kukhala okonzeka.
Nanga, kodi tsogolo lanu lidzakhala bwanji? Kodi pali amene angadziŵe? Zina zimene akatswili amalosela zimacitika, koma zambili sizimacitika. Mosiyana ndi anthuwa, Mulungu amalosela ndendende zimene zidzacitika mtsogolo. Mau ake amati: “Ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi. Kuyambila kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinacitike.” (Yesaya 46:10) Kodi zimene Mulungu amanena zimacitikadi?
ZIMENE MULUNGU AMANENA ZIMACITIKADI
N’cifukwa ciani muyenela kucita cidwi ndi mmene maulosi a Mulungu anakwanilitsidwila m’nthawi zakale? Ngati munthu amene amadziŵa zanyengo wakhala wodalilika kwa nthawi yaitali mungam’dalile. Mwacionekele, mudzatsimikiza zimene adzakuuzani zokhudza mmene nyengo idzakhalila tsiku lotsatila. Mofananamo, mukadziŵa kuti zimene Mulungu analosela zinacitikadi, mudzakhulupilila kuti zimene amatiuza ponena za mtsogolo zidzacitikadi.
KUONONGEDWA KWA MZINDA WAUKULU:
Mwacitsanzo, kulosela ndendende kuti mzinda waukulu, umene kwa nthawi yaitali unali wolimba udzaonongedwa cinali cinthu cocititsa cidwi. Mulungu kudzela mwa womulankhulila, analosela za kuonongedwa kwa mzinda wa Nineve. (Zefaniya 2:13-15) Kodi akatswili a mbili yakale atulukila ciani? Iwo anapeza umboni wosonyeza kuti m’zaka za m’ma 600 B.C.E., patapita zaka 15 kucokela pamene Mulungu analosela za kuonongedwa kwa mzindawu, Ababulo ndi Amedi anauononga ndi kuulanda. Ndipo Mulungu ananenelatu kuti mzindawu udzakhala ‘bwinja, ndi wopanda madzi ngati cipululu.’ Kodi ulosi umenewu unakwanilitsika? Inde. Mzindawu pamodzi ndi midzi yozungulila unali waukulu mwina makilomita 518 mbali zonse zinayi. Ngakhale n’conco, anthu amene anagonjetsa anthu okhala mum’zindamo sanafune kuulanda ndi kukhalamo monga mmene ena anaganizila. M’malo mwake anaunonga. Kodi ndi katswili wa zandale uti amene akanalosela ndendende zocitikazi?
ADZAOCHA MAFUPA A ANTHU:
Kodi ndani akanalosela ndendende za makolo amene anali kudzabeleka mwana amene anali kudzaocha mafupa a anthu pa guwa la nsembe? Ndani akanalosela za tauni kumene guwa la nsembe linali kudzamangidwila zaka 300 zimenezi zisanacitike? Kukwanilitsidwa kwa ulosi wa conco kukanacititsa kuti woloselayo adziŵike. Wolankhulila Mulungu analosela kuti: “Mwana wamwamuna adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake Yosiya . . . Iye adzaocha mafupa a anthu” pa guwa la nsembe m’tauni yochedwa Beteli. (1 Mafumu. 13:1, 2) Pafupifupi zaka 300 izi zitaloseledwa, Mfumu Yosiya anaonekela m’banja la Davide. Mofanana ndi zimene zinaloseledwa, Yosiya anatumiza anthu kuti “akatenge mafupa m’mandawo, ndipo anawatentha paguwa lansembelo” ku Beteli (2 Mafumu. 23:14-16) Kodi munthu wina akanakwanitsa bwanji kulosela zinthu zimenezi popanda kuthandizidwa ndi munthu wamphamvu kuposa ena onse?
KUTHA KWA UFUMU:
Cikanakhala cinthu codabwitsa ngati munthu akanalosela ndendende za munthu ndi dzina lake amene akanatsogolela kukagonjetsa ufumu wapadziko lonse, ndi njila yacilendo imene munthuyo akanacitila zimenezo nthawi yaitali zimenezo zisanacitike. Mulungu analosela kuti Koresi anali kudzagonjetsa mitundu ya anthu, kudzamasula Ayuda mu ukapolo, ndi kuwacilikiza panchito yomanganso kacisi woyela. Analoselanso kuti Koresi anali kudzaphwetsa madzi a mtsinje umene unali kudutsa mumzinda wa Babulo ndi kuti adzapeza kuti zitseko za mzindawo n’zosatseka. Zimenezi zinacititsa kuti Koresi aononge mzindawo mosavuta. (Yesaya 44:27–45:2) Kodi zimene Mulungu analosela zinakwanilitsidwadi? Akatswili a mbili yakale amacitila umboni kuti Koresi anaonongadi mzinda wa Babulo. Asilikali a Koresi anagwilitsila nchito njila yaluso popatutsa madzi a mtsinje wodutsa mumzinda wa Babulo ndipo mtsinjewo unauma. Iwo analoŵa mumzinda pa zipata zimene zinasiidwa zosatseka. Kenako, Koresi anamasula Ayuda ndi kuwauza kuti akamangenso kacisi wao ku Yerusalemu. Zimene Koresi anacita zinali zacilendo cifukwa iye sanali kulambila Mulungu wa Ayuda. (Ezara 1:1-3) Mulungu ndi yekhayo amene akanalosela ulosiwu.
Tafotokoza zocitika zitatu zosonyeza mmene Mulungu analoselela zinthu zamtsogolo mwatsatanetsatane. Koma palinso zinthu zina zimene Mulungu analosela. Yoswa, mtsogoleli wa Ayuda, ananena za zinthu zimene anthuwo anali kudziŵa bwino kuti: “Inu mukudziŵa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pa mau onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwanilitsidwe. Onse akwanilitsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mau amodzi omwe sanakwanilitsidwe.” (Yoswa 23:1, 2, 14) Ayuda sanatsutse kuti Mulungu anakwanilitsa malonjezo ake. Koma kodi Mulungu amakwanilitsa bwanji malonjezo ake? Mmene Mulungu amacitila zinthu zimasiyana kwambili ndi anthu. Muyenela kudziŵa zimenezi cifukwa cakuti Mulungu wapeleka malonjezo ambili okhudza zamtsogolo amene adzakukhudzani.
MAULOSI A MULUNGU AMASIYANA NDI A ANTHU
Nthawi zambili anthu amalosela zinthu zozikidwa pa kafukufuku wa sayansi, maumboni a zinthu zina, kusintha kwa zinthu, kapena pa mauthenga abodza onenedwa ndi Akristu onama. Anthu akalosela amangoyembekezela kuti aone ngati zimene alosela zidzacitikadi.—Miyambo 27:1.
Mosiyana ndi anthu, Mulungu amadziŵa zonse. Iye adziŵa bwino cibadwa ca anthu ndi maganizo ao. Conco, akalosela amadziŵa bwino mmene anthu adzakwanilitsila maulosi ake. Ndiponso, Mulungu ali ndi mphamvu ndipo angasinthe zinthu kuti zimene walosela zikwanilitsike mmene iye afunila. Iye anati: “Mau otuluka pakamwa panga . . . sadzabwelela kwa ine popanda kukwanilitsa colinga cake, . . . ndipo adzakwanilitsadi zimene ndinawatumizila.” (Yesaya 55:11) Maulosi a Mulungu amatiuza zimene zidzacitika mtsogolo. Mulungu amatiuzanso za maulosi amene anakwanilitsidwa kale.
TSOGOLO LANU
Kodi pali ulosi wodalilika umene umakhudza tsogolo lanu ndi la acibale anu? Ngati mungadziŵe pasadakhale kuti kudzabwela cimphepo coononga mungacitepo kanthu kuti mudzapulumuke. Mofananamo muyenela kukonzekela zinthu zimene zidzacitika mogwilizana ndi ulosi wa m’Baibulo. Mulungu analosela kuti posacedwapa zinthu padzikoli zidzasintha kwambili. (Onani bokosi lakuti: “Zimene Mulungu Walosela.”) Zimene zidzacitika mtsogolo zidzakhala zosiyana kwambili ndi zimene anthu ambili amalosela.
Mwina zimenezi zidzacitika mwanjila iyi: Anthu onse akuyembekeza zinthu zimene zidzawakhudza mtsogolo. Zinthuzo zalembedwa kale ndipo akudziŵa mmene zidzacitikila. Mulungu analonjeza kuti: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi . . . Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalila zanga zidzacitikadi, ndipo ndidzacita ciliconse cimene ndikufuna.’” (Yesaya 46:10) Inuyo ndi banja lanu mungakhale ndi tsogolo labwino. Funsani Mboni za Yehova kuti zikuuzeni zimene Baibulo limanena zokhudza zocitika zamtsogolo. Mboni za Yehova sizimaona zamtsogolo, kumva mau ocokela ku mizimu kapena kulosela zamtsogolo. Iwo amaphunzila Baibulo ndipo adzakuuzani zinthu zabwino zimene Mulungu walonjeza kuti adzacita mtsogolo.