NKHANI YA PACIKUTO | KODI NDANI AMADZIŴADI ZAMTSOGOLO?
Zimene Ena Amalosela Zimacitika, Koma Zambili Sizimacitika
Kodi mufuna kudziŵa za tsogolo lanu? Ambili amatelo, ndipo ena amalosela za mtsogolo. Komabe pamakhala zotsatilapo zosiyanasiyana. Ganizilani zitsanzo zotsatilazi:
ASAYANSI amagwilitsila nchito zipangizo ndi ndalama zambili kuti adziŵe zamtsogolo. Mwacitsanzo, amafuna kudziŵa mmene kuonongedwa kwa mpweya kudzakhudzila dziko lapansi. Amafunanso kudziŵa ngati mvula idzagwa kudela lanu tsiku lotsatila.
AKATSWILI OFUFUZA amalosela mmene malonda ndi ndale zidzayendela. Warren Buffett, mmodzi mwa anthu olemela padziko lonse lapansi, amalosela zamalonda molondola cakuti anthu ena amamucha kuti ndi mneneli. Katswili wina wofufuza wochedwa Nate Silver, amagwilitsila nchito malipoti ocokela kwa anthu kuti am’thandize kulosela zilizonse monga mmene ndale zidzayendela m’dziko la U.S., kapena amene adzalandila mphoto pa zamafilimu a ku Hollywood.
MABUKU NDI ZOLEMBA ZAKALE zimaonedwa kuti zili ndi maulosi. Anthu ena aona kuti zimene Michel de Notredame (Nostradamus) analemba m’zaka za m’ma 1500 zikukwanilitsidwa masiku ano. Anthu ena anaona kuti kalendala ya Mayan imene inatha pa December 21, 2012 inali ndi cenjezo la zocitika zoopsa.
ATSOGOLELI ACIPEMBEDZO nthawi zina amalosela zocitika zoopsa za padziko lapansi kuti acenjeze anthu ndi kusonkhanitsa otsatila ao. Harold Camping, amene amalosela za kuonongedwa kwa dziko, analengeza pamodzi ndi ophunzila ake kuti dziko lapansi lidzaonongedwa mu 2011. Koma zimenezi sizinacitike.
ANTHU OLOSELA ZAMTSOGOLO amanena kuti ali ndi mphamvu yodziŵa zamtsogolo. Edgar Cayce ndi Jeane Dixon analosela molondola zimene zinacitika m’zaka za m’ma 1900. Koma zambili zimene io analosela sizinacitike. Mwacitsanzo, Dixon analosela kuti Nkhondo Yacitatu ya Dziko lonse idzayamba mu 1958, ndipo Cayce analosela kuti mu 1975 mzinda wa New York udzamizidwa ndi madzi.
Muyenela kudzifunsa kuti: Kodi pali njila yodalilika imene ndingadziŵile zamtsogolo? Kudziŵa za mtsogolo kungakuthandizeni kusankha bwino zinthu pa umoyo wanu.