LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/15 masa. 23-27
  • “Inu Ndinu Mboni Zanga”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Inu Ndinu Mboni Zanga”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MBONI ZA MULUNGU M’NTHAWI YAKALE
  • “TAONANI! NDIKUPANGA ZINTHU ZATSOPANO”
  • CIMENE DZINA LA MULUNGU LITANTHAUZA
  • TIZIONETSA KUTI TIMAYAMIKILA
  • Yehova Akweza Dzina Lake
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Ife?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Ni Cifukwa Ciani Timachedwa Mboni za Yehova?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Kodi Dzina la Mulungu N’ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/15 masa. 23-27

“Inu Ndinu Mboni Zanga”

“‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutelo Yehova.”—YES. 43:10.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Aisiraeli anakhala mboni za Yehova m’njila ziti?

  • Kodi dzina la Mulungu lingatanthauzenji?

  • Nanga tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwai wodziŵika ndi dzina la Mulungu loyela?

1, 2. (a) Kodi kukhala mboni kumatanthauza ciani? Nanga amtolankhani a dziko alephela m’njila ziti? (b) N’cifukwa ciani Yehova sadalila amtolankhani a dziko?

KODI kukhala mboni kumatanthauza ciani? Dikishonale ina imati: “Ndi munthu amene waona cocitika cinacake ndipo auzako ena cocitikaco.” Mwacitsanzo, mumzinda wa Pietermaritzburg, ku South Africa, nyuzipepala ina imene imachedwa kuti The Witness yakhala ikufalitsidwa kwa zaka 160 tsopano. Dzina limeneli ndi loyenelela cifukwa colinga ca nyuzipepala imeneyi ndico kuuzako ena zenizeni zimene zimacitika. Woyambitsa nyuzipepala imeneyi, analonjeza kuti zolembedwa zake zizikhala “zoona zokhazokha basi.”

2 Koma n’zacisoni kuti amtolankhani ambili a m’dzikoli amanyalanyaza kuuza anthu nkhani zofunika kwambili za mbili ya anthu. Zimenezi n’zimene Mulungu wamphamvuyonse ananena kupyolela mwa mneneli wake wakale Ezekieli, kuti: “Mitundu ina ya anthu idzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” (Ezek. 39:7) Koma Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse sadalila amtolankhani kudziŵitsa anthu za iye. Iye ali ndi Mboni zokwana 8 miliyoni zimene zimauza anthu a mitundu yonse zimene anacitila anthu kale, ndi zimene akuwacitila tsopano. Gulu la Mboni limeneli limalengeza zimene Mulungu walonjeza kudzacitila anthu mtsogolo. Mwa kuika nchito yocitila umboni patsogolo, timayamikila dzina lathu lopatsidwa ndi Mulungu mogwilizana ndi Yesaya 43:10 limene limati: “‘Inu ndinu mboni zanga,” akutelo Yehova. “Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani.’”

3, 4. (a) Ndi liti pamene Ophunzila Baibulo anayamba kudziŵika ndi dzina latsopano? Ndipo anamva bwanji cifukwa ca dzinalo? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Nanga ndi mafunso ati amene tikambilane?

3 Ndi mwai waukulu kudziŵika ndi dzina la Yehova, cifukwa iye ndi “Mfumu yamuyaya.” Iye amati: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale, ndipo ndico condikumbukilila ku mibadwomibadwo.” (1 Tim. 1:17; Eks. 3:15; yelekezelani ndi Mlaliki 2:16.) Mu 1931, Ophunzila Baibulo anasankha kudziŵika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova. Pambuyo pake, makalata oyamikila anaikidwa m’magazini a mwezi umenewo. Mpingo wina wa ku Canada unalemba kuti: “Nkhani yakuti ndife ‘mboni za Yehova’ yatikondweletsa kwambili, ndipo yaticititsa kukhala ofunitsitsa kucita zinthu mogwilizana ndi dzina lathu latsopano.”

4 Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwai wodziŵika ndi dzina la Mulungu? Kodi tingafotokoze nkhani ya pa Lemba limene dzina lathu lakuti Mboni za Yehova licokela?

MBONI ZA MULUNGU M’NTHAWI YAKALE

5, 6. (a) Kodi makolo aciisiraeli anali mboni za Yehova m’njila ziti? (b) N’ciani cina cimene analamulidwa kucita? Ndipo n’cifukwa ciani malangizo amenewo amagwilanso nchito kwa makolo masiku ano?

5 Aisiraeli a m’nthawi ya Yesaya anali “mboni “ za Yehova, ndipo monga gulu anali “atumiki” a Mulungu. (Yes. 43:10) Njila imodzi imene makolo aciisiraeli anacitila umboni, inali mwa kuphunzitsa ana ao zimene Mulungu anacitila makolo akale. Mwacitsanzo, pankhani yocita Pasika caka ciliconse, anthuwo anauzidwa kuti: “Ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza ciani?’ pamenepo mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopeleka nsembe ya Pasika kwa Yehova, amene anapitilila nyumba za ana a Isiraeli mu Iguputo pamene anali kupha Aiguputo ndi mlili, koma anapulumutsa mabanja athu.’” (Eks. 12:26, 27) Makolowo anafotokozelanso ana ao mmene zinalili pamene Mose kwa nthawi yoyamba, anaonekela kwa mfumu ya Iguputo. Iye anapita kukapempha mfumuyo kuti ilole Aisiraeli kuti apite kukalambila Yehova m’cipululu, ndipo Farao anayankha kuti: “Yehova ndani kuti ndimvele mau ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?” (Eks. 5:2) Mwina anauzanso ana ao kuti pambuyo pakuti milili 10 yaononga Iguputo, ndi pamene Aiguputo analephela kugwila Aisiraeli pa Nyanja Yofiila, yankho la funso la Farao linayankhidwa bwino. Zinadziŵika kuti Yehova ndiye Wamphamvuyonse. Ndiponso, Aisiraeli anakhala mboni zakuti Yehova ndiye Mulungu woona ndi kuti amakwanilitsa malonjezo ake.

6 Aisiraeli amene anayamikila mwai wodziŵika ndi dzina la Yehova, mwacionekele anauzako ana ao ndi alendo amene anali akapolo ao, zinthu zimene Mulungu anacita. Aisiraeli anafunikilanso kuphunzitsa ana ao kutsatila miyezo yoyela ya Mulungu. Yehova anati: “Mukhale oyela, cifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyela.” (Lev. 19:2; Deut. 6:6, 7) Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwa makolo acikristu masiku ano. Makolo ayenela kuphunzitsa ana ao kutsatila njila zoyela, ndi kuwathandiza kulemekeza dzina lolemekezeka la Mulungu.—Ŵelengani Miyambo 1:8; Aefeso 6:4.

7. (a) Pamene Isiraeli anali wokhulupilika kwa Yehova, kodi mitundu yowazungulila inakhudzidwa motani? (b) Kodi onse amene amadziŵika ndi dzina la Mulungu ali ndi udindo wotani?

7 Conco, pamene Aisiraeli anali okhulupilika, anacitila umboni dzina la Mulungu mokwanila. Iwo anauzidwa kuti: “Mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukuchedwa ndi dzina la Yehova, ndipo adzacita nanu mantha.” (Deut. 28:10) Komabe, n’zacisoni kuti nthawi zambili Aisiraeli sanali okhulupilika. Nthawi ndi nthawi, anali kubwelelanso kukalambila mafano opangidwa ndi anthu. Ndiponso, mofanana ndi milungu yacikanani imene anali kulambila, io anakhala anthu ankhanza, anayamba kupeleka ana ao nsembe ndipo anali kupondeleza osauka. Limeneli ndi phunzilo lofunika kwambili kwa ife. Nthawi zonse tiyenela kuyesetsa kukhala oyela potsatila Woyela Koposa, mwini dzina limene timadziŵika nalo.

“TAONANI! NDIKUPANGA ZINTHU ZATSOPANO”

8. Ndi nchito yotani imene Yehova anapatsa Yesaya? Nanga Yesaya anailandila bwanji?

8 Yehova anakambilatu kuti Aisiraeli adzacitila umboni za kumasulidwa mocititsa cidwi ku ukapolo. (Yes. 43:19) Macaputala 6 oyambilila a buku la Yesaya, anapeleka cenjezo la masoka amene anali kudzagwela Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulila. Yehova amene amaona mitima, anauza Yesaya kupitilizabe kulengeza cenjezo limeneli ngakhale kuti ena sadzamvela. Yesaya anadabwa nazo zimenezi ndipo anafuna kudziŵa kuti mtundu wosankhidwa wa Mulungu udzakhalabe wosalapa kwautali wotani. Mulungu anayankha kuti: “Mpaka mizinda yao itaonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zao zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itaonongekelatu.”—Ŵelengani Yesaya 6:8-11.

9. (a) Ulosi wa Yesaya wokhudza Yerusalemu unakwanilitsidwa liti? (b) Nanga n’ciani cikucitika masiku ano cimene cingafune kuti tikhale maso?

9 Yesaya anapatsidwa nchito imeneyi m’caka cothela ca ulamulilo wa Mfumu Uziya, kapena kuti mu 778 B.C.E. Anapitilizabe kutumikila monga mneneli kwa zaka 46, mpaka mu ulamulilo wa Mfumu Hezekiya mu 732 B.C.E. Zimenezi zinacitika zaka 125 Yerusalemu asanaonongedwe mu 607 B.C.E. Conco, anthu a Mulungu anauzidwa pasadakhale zimene zinali kudzawacitikila mtsogolo. Ngakhale masiku ano, Yehova amauzilatu anthu ake pasadakhale zimene zidzacitika mtsogolo. Kwa zaka 135, kuyambila pamene Nsanja ya Mlonda inayamba kufalitsidwa, yakhala ikucenjeza aŵelengi ake kuti ulamulilo woipa wa Satana udzatha, ndipo udzaloŵedwa m’malo ndi Ulamulilo wa Zaka 1000 wa Yesu Kristu.—Chiv. 20:1-3, 6.

10, 11. Pamene Aisiraeli anali ku Babulo, kodi anaona kukwanilitsika kwa ulosi uti wa Yesaya?

10 Ayuda okhulupilika ambili amene anagwidwa ndi a Babulo anapulumuka pamene Yerusalemu anaonongedwa, ndipo anatengedwa ku ukapolo ku Babulo. (Yer. 27:11,12) Patapita zaka 70, anthu a Mulungu amene anali kumeneko anaonako pamene ulosi wodabwitsa unakwanilitsidwa wakuti: “Yehova, Wokuombolani, Woyela wa Isiraeli wanena kuti: ‘Cifukwa ca inu, ndidzawatumiza ku Babulo. Ndidzacititsa kuti zitsulo za ndende zimasuke.’”—Yes. 43:14.

11 Mogwilizana ndi ulosi umenewu, kuciyambi kwa October, 539 B.C.E. usiku, kunacitika cinthu cimene cinagwedeza dziko lonse. Amedi ndi Aperisiya anagonjetsa Babulo pamene Mfumu ya Babulo ndi akazembe ake, anali kumwa vinyo m’ziwiya zoyela zimene anatenga m’kacisi ku Yerusalemu, ndi pamene anali kulambila milungu yao yopangidwa ndi anthu. Mu 538 kapena mu 537 B.C.E., Koresi analamula Ayuda kuti abwelele kwao kukamanganso kacisi wa Mulungu ku Yerusalemu. Yesaya ndiye analemba zinthu zonsezi. Ndipo analembanso za lonjezo la Yehova lakuti adzasamalila anthu ake ndi kuwateteza akadzabwelela ku Yerusalemu. Mulungu anawacha kuti “anthu anga amene ndawapanga kuti akhale anga, anene za ulemelelo wanga.” (Yes. 43:21; 44:26-28) Pamene anthuwa anabwelela kukamanganso kacisi wa Yehova ku Yerusalemu, anakhala mboni pankhani yakuti Yehova, Mulungu yekha woona, amakwanilitsa mau ake nthawi zonse.

12, 13. (a) Ndani anali pakati pa Aisiraeli pamene io anayambanso kulambila Yehova? (b) Kodi “nkhosa zina” ziyenela kucitanji pothandiza “Isiraeli wa Mulungu”? Ndipo zili ndi ciyembekezo cotani?

12 Anthu ambili amene sanali Aisiraeli anakhala mbali ya mtundu wobadwanso wa Ayuda, ndipo patapita nthawi anthu ena akunja anatengela zikhulupililo za Ayuda. (Ezara 2:58, 64, 65; Estere 8:17) Masiku ano, a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Yesu, amacilikiza mokhulupilika Akristu odzozedwa amene ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Chiv. 7:9, 10; Yoh. 10:16; Agal. 6:16) A khamu lalikulu naonso ali ndi dzina lopatsidwa ndi Mulungu lakuti Mboni za Yehova.

13 Mu ulamulilo wa Kristu wa zaka 1000, a khamu lalikulu adzakondwela kufotokozela anthu amene adzaukitsidwa mmene zinalili kukhala Mboni ya Yehova m’masiku otsiliza. Koma tingacite zimenezi kokha ngati timacita zinthu mogwilizana ndi dzina lathu ndi kukhalabe oyela. Ndiponso, kaya tiyesetse bwanji, tsiku lililonse tifunikila kupempha cikhululukilo cifukwa ca cidetso ciliconse. Ndipo tiyenela kuzindikila kuti ndife ocimwa, ndi kuti kudziŵika ndi dzina loyela la Mulungu ndi mwai waukulu.—Ŵelengani 1 Yohane 1:8, 9.

CIMENE DZINA LA MULUNGU LITANTHAUZA

14. Kodi dzina lakuti Yehova lingatanthauzenji?

14 Kuti tiyamikile kwambili mwai wokhala ndi dzina la Mulungu, tiyenela kuganizila kwambili tanthauzo la dzina lake. Dzina la Mulungu lakuti “Yehova,” licokela ku mau aciheberi amene atanthauza “Kukhala.” Conco, dzina lakuti Yehova lingatanthauze kuti “Amacititsa Kukhala.” Tanthauzo limeneli limuyenelela Yehova popeza ndi Mlengi wacilengedwe conse ndi wokwanilitsa malonjezo. Pamene zinthuzi zikucitika, Iye wapitilizabe kucititsa kuti cifuno cake cikwanilitsidwe mosasamala kanthu ndi zimene wotsutsa aliyense, monga Satana, angacite kuti alepheletse kukwanilitsidwa kwa cifunilo ca Mulungu.

15. Tiphunzilapo ciani pa zimene Yehova anauza Mose ponena za tanthauzo la dzina lake? (Onani bokosi lakuti, “Dzina Limene Lili ndi Tanthauzo Kwambili.”)

15 Pamene Yehova anatuma Mose kukatulutsa anthu ake mu Iguputo, Iye anauza Mose mbali ina ya umunthu wake. Iye anauza Mose mwacindunji tanthauzo la dzina lake. Baibulo limati: “Mulungu anamuyankha Mose kuti: ‘Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.’ Ndiyeno anaonjezela kuti: ‘Ana a Isiraeli ukawauze kuti “Ndidzakhala Amene Ndidzafuna Kukhala ndiye wandituma kwa inu.”’” (Eks. 3:14) Conco, mosasamala kanthu ndi zilizonse, Yehova adzakhala ciliconse cofunikila kuti akwanilitse cifunilo cake. Kwa Aisiraeli amene anali ku ukapolo, iye anakhala Mpulumutsi, Mtetezi, Mtsogoleli, ndi wosamalila zosoŵa zao zonse zakuthupi ndi zakuuzimu.

TIZIONETSA KUTI TIMAYAMIKILA

16, 17. (a) Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwai wodziŵika ndi dzina la Mulungu? (b) Tidzakambitsilana ciani m’nkhani yotsatila?

16 Masiku ano, Yehova wapitilizabe kucita zinthu mogwilizana ndi dzina lake, mwa kusamalila zosoŵa zathu zakuthupi, ndi zakuuzimu. Komabe, dzina la Mulungu silimangotanthauza kuti iye amacititsa kuti kukhale. Koma limatanthauzanso zimene iye amacita zokhudza nchito imene Mboni zake zimacita kuti akwanilitse cifunilo cake. Kuganizila kwambili zimenezi kumatilimbikitsa kupitilizabe kukhala mogwilizana ndi dzina lathu. Mboni ina yokangalika ya zaka 84 ya ku Norway dzina lake Kåre inati: “Ndimaona kuti ndi mwai waukulu kutumikila Yehova, Mfumu yacilengedwe conse, ndi kukhala pakati pa anthu odziŵika ndi dzina lake loyela. Ndi mwai waukulu kuuza anthu coonadi ca Baibulo ndi kuwaona akucimvetsetsa. Mwacitsanzo, ndimakondwela kuphunzitsa anthu kuti adziŵe mmene nsembe ya dipo ya Kristu imagwilila nchito, ndi mmene idzatithandizila kukhala ndi moyo wosatha m’dziko la mtendele ndi lolungama.”

17 N’zoona kuti m’magawo ena n’zovuta kupeza anthu ofuna kuphunzila za Mulungu. Komabe, mofanana ndi Kare, kodi mumakondwela mukapeza munthu wofuna kuphunzila? Nanga mumaphunzitsako ena za dzina la Yehova? Komabe, tingakhale bwanji Mboni za Yehova ndi za Yesu panthawi imodzi? Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila.

Dzina Limene Lili ndi Tanthauzo Kwambili

Zimene limatanthauza

  • “Iye Amacititsa Kuti Kukhale”

Cifukwa cake ndi loyenelela

  • Yehova analenga zinthu zonse

  • Iye wapitilizabe kucititsa kuti cifunilo cake cikwanilitsidwe

Zimene limavumbula

  • Iye adzakhala ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse cifunilo cake

  • Amapangitsa cilengedwe cake kucita ciliconse cimene afuna kuti akwanilitse cifunilo cake

  • Sangalephele kucita ciliconse kapena kupangitsa ciliconse kucitika kuti akwanilitse cifunilo cake

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani