LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 May masa. 26-31
  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Ife?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Ife?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LAKE”
  • “INU NDINU MBONI ZANGA”
  • MMENE TIMAONETSELA KUTI DZINA LA YEHOVA N’LOFUNIKA KWA IFE
  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Yesu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • “Tamandani Dzina la Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • “Sankhani . . . Amene Mukufuna Kum’tumikila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 May masa. 26-31

NKHANI YOPHUNZILA 23

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Ife?

“‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutelo Yehova.”​—YES. 43:10.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Udindo umene tili nawo poyeletsa ndi kukweza dzina la Yehova.

1-2. Kodi timadziwa bwanji kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwa Yesu?

DZINA la Yehova ndi lofunika kwambili kwa Yesu kuposa cina ciliconse. Ndiye ali patsogolo pa nkhani yoyeletsa ndi kukweza dzina la Atate wake. Monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yesu anali wokonzeka kufa cifukwa ca dzina la Yehova komanso cifukwa ca zonse zimene dzinalo limaimila. (Maliko 14:36; Aheb. 10:​7-9) Pambuyo pa ulamulilo wake wa zaka 1,000, Yesu adzakhala wokonzeka kutula pansi ulamulilo wake wonse kuti ulemelelo wonse upite kwa Yehova. (1 Akor. 15:​26-28) Zonse zimene Yesu wacitila Yehova zimaonetsa kuti iye amakonda Yehova kwambili.

2 Yesu anabwela padziko lapansi m’dzina la Atate wake. (Yoh. 5:43; 12:13) Anadziwikitsa dzina la Atate wake kwa otsatila ake. (Yoh. 17:​6, 26) Anali kuphunzitsa m’dzina la Yehova ndi kucita zozizwitsa m’dzinalo. (Yoh. 10:25) Ndipo pamene Yesu anapempha Yehova kuti ayang’anile ophunzila ake, anapempha Yehova kuti acite zimenezo “cifukwa ca dzina [Lake].” (Yoh. 17:11) Ndiye ngati umu ndi mmene Yesu anali kulikondela dzina la Yehova, kodi zingatheke bwanji munthu kukamba kuti ndi wotsatila weniweni wa Khristu ngati salidziwa dzinalo kapena kuligwilitsa nchito?

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Pokhala Akhristu amene amayesetsa kutsatila mapazi a Yesu, timalikonda dzina la Atate wake ndi kulilemekeza. (1 Pet. 2:21) M’nkhani ino tiphunzila cifukwa cake anthu amene amalalikila “uthenga wabwino . . . wa Ufumu” amachedwa ndi dzina la Yehova. (Mat. 24:14) Tikambilanenso mmene aliyense wa ife ayenela kulionela dzina la Yehova.

“ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LAKE”

4. (a) Kodi Yesu anapatsa ophunzila ake nchito yotani asanabwelele kumwamba? (b) Nanga zimenezi zimadzetsa funso lotani?

4 Yesu atatsala pang’ono kubwelela kumwamba anauza ophunzila ake kuti, “Mukadzalandila mzimu woyela mudzakhala ndi mphamvu ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Conco uthenga wabwino unali kudzalalikidwa m’madela onse osati mu Isiraeli mokha. M’kupita kwa nthawi, anthu amitundu yonse anali kudzakhala ndi mwayi wokhala otsatila a Yesu. (Mat. 28:​19, 20) Koma onani kuti Yesu anati: “Mudzakhala mboni zanga.” Kodi ophunzila atsopano amenewo anafunikila kudziwa dzina la Yehova kapena anali kudzangokhala mboni za Yesu? Nkhani ya pa Machitidwe caputala 15 imayankha funsoli.

5. Kodi atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anaonetsa bwanji kuti anthu ayenela kudziwa dzina la Yehova? (Onaninso cithunzi.)

5 Mu 49 C.E., atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anakumana kuti akambilane zimene anthu amitundu ina osadulidwa anayenela kucita kuti akhale Akhristu. Kumapeto kwa makambilanowo, Yakobo m’bale wake wa Yesu ananena kuti: “[Petulo] wafotokoza bwino mmene Mulungu anaceukila anthu amitundu ina kwa nthawi yoyamba kuti pakati pawo atengepo anthu odziwika ndi dzina lake.” Kodi Yakobo anali kukamba dzina la ndani? Pogwila mawu a mneneli Amosi, iye anapitiliza kuti: “Ndidzacita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova ndi mtima wonse, amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu ochedwa ndi dzina langa, watelo Yehova.” (Mac. 15:​14-18) Kuwonjezela pa kuphunzila za Yehova, ophunzila atsopanowo anali ‘kudzadziwika ndi dzina lake.’ Izi zitanthauza kuti anali kudzadziwitsa dzina la Mulungu kwa ena ndipo anthuwo anali kudzadziwa kuti iwo amaimilako dzinalo.

Yakobo akukambilana ndi ena mwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. Awili mwa abalewo ali ndi mipukutu yotseguka pomwe akumvetsela.

Pa miting’i yawo, amuna okhulupilika am’bungwe lolamulila la m’nthawi ya atumwi anazindikila kuti Akhristu ayenela kukhala anthu odziwika ndi dzina la Mulungu (Onani ndime 5)


6-7. (a) N’cifukwa ciyani Yesu anabwela padziko lapansi? (b) Nanga cofunika koposa cimene anabwelela padziko lapansi cinali ciyani?

6 Dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndi Cipulumutso,” ndipo Yehova anagwilitsa nchito Yesu kuti apulumutse onse okhala ndi cikhulupililo. Yesu anabwela padziko lapansi kudzapeleka moyo wake kuti apulumutse mtundu wa anthu. (Mat. 20:28) Mwa kupeleka dipo, Yesu anatheketsa kuti mtundu wa anthu upulumutsidwe ndi kukapeza moyo wosatha.​—Yoh. 3:16.

7 Koma kodi n’cifukwa ciyani mtundu wa anthu unayenela kupulumutsidwa? Cinali cifukwa ca zimene zinacitika m’munda wa Edeni. Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, makolo athu oyambilila, Adamu ndi Hava, anapandukila Yehova n’kutaya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. (Gen. 3:​6, 24) Yesu anabwela padziko lapansi kudzapulumutsa mtundu wa anthu. Koma panalinso cina cofunika koposa cimene anabwelela. Kumbukilani kuti dzina la Yehova linali litadetsedwa. (Gen. 3:​4, 5) Conco, cipulumutso ca mbadwa za Adamu ndi Hava cinali kukhudzana ndi nkhani yaikulu yomwe ndi kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova. Cifukwa cakuti Yesu amaimilako Yehova ndipo amadziwika ndi dzina lake, anacita mbali yaikulu poyeletsa dzina la Yehova.

Kodi zingatheke bwanji munthu kukamba kuti ndi wotsatila weniweni wa Khristu ngati salidziwa dzina la Atate wake ndi kuligwilitsa nchito?

8. Kodi okhulupilila onse a Yesu anafunika kuzindikila ciyani?

8 Ayuda komanso anthu amitundu ina amene anakhulupilila Yesu anafunikila kuzindikila kuti Gwelo la cipulumutso cawo ndi Yehova Mulungu, Atate wake wa Yesu. (Yoh. 17:3) Kuwonjezela apo, monga zinalili ndi Yesu, iwonso anali kudzayamba kudziwika ndi dzina la Yehova. Cina, iwo anafunikilanso kudziwa kufunika kwa kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova. M’pamene panagona cipulumutso cawo. (Mac. 2:​21, 22) Conco, otsatila onse a Yesu anayenela kuphunzila za Yehova komanso za Yesu. M’pake kuti Yesu anamaliza pemphelo lake la mu Yohane 17 ndi mawu akuti: “Ine ndacititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziwitsa dzinalo kuti iwonso azisonyeza cikondi ngati cimene inu munandisonyeza, kuti inenso ndikhale wogwilizana ndi iwo.”​—Yoh. 17:26.

“INU NDINU MBONI ZANGA”

9. Kodi tingaonetse motani kuti dzina la Yehova n’lofunika kwa ife?

9 Otsatila onse enieni a Yesu ali ndi udindo woyeletsa dzina la Yehova. (Mat. 6:​9, 10) Iwo ayenela kuona dzina la Yehova kuti ndi lokwezeka kwambili kuposa cina ciliconse. Ayenela kutelo m’zocita zawo. Koma kodi tingaliyeletse motani dzina la Yehova, kapena kuti kucotsa zitonzo zimene Satana waunjika pa dzinalo?

10. Mophiphilitsa, kodi Yesaya 42 mpaka 44 imafotokoza nkhani iti imene ili ku khoti? (Yesaya 43:9; 44:​7-9) (Onaninso cithunzi.)

10 Kufunika kwa udindo wathu woyeletsa dzina la Yehova kunafotokozedwa mu Yesaya caputala 42 mpaka 44. Mophiphilitsa, macaputala amenewa amafotokoza nkhani imene ili ku khoti yokamba za umulungu. Yehova akuuza onse amene amanena kuti ndi milungu kuti apeleke umboni wotsimikizila kuti ndi milungudi. Akuuzanso mboni kuti zipeleke umboni wotsimikizila umulungu wawo. Koma palibe akukwanitsa kutelo!​—Welengani Yesaya 43:9; 44:​7-9.

Zithunzi: Angelo akuuluka mumlengalenga pafupi ndi dziko lapansi pomwe abale ndi alongo padziko lonse akutengapo gawo poyeletsa dzina la Yehova. 1. Mwamuna ndi mkazi wake akucita ulaliki wapakasitandi. 2. Mlongo wacitsikana akupeleka khadi lolowela pa jw.org kwa mnzake wakusukulu. 3. M’bale akulalikila kwa mwamuna m’basi. 4. M’bale wamangidwa ndipo akutengedwa ndi apolisi ovala mamasiki. 5. Mlongo wagonekedwa m’cipatala ndipo akuuza dokotala maganizo ake pankhani ya magazi.

Timaonetsa kuti palibe Mulungu wina kupatulapo Yehova m’zonse zimene timakamba ndi kucita (Onani ndime 10-11)


11. Malinga ndi Yesaya 43:​10-12, n’cilengezo cotani cimene Yehova akupeleka kwa anthu ake?

11 Welengani Yesaya 43:​10-12. Ponena za anthu ake, Yehova akunena kuti: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndipo ine ndine Mulungu.” Yehova akupempha anthu akewo kuyankha funso lakuti: “Kodi palinso Mulungu wina kupatulapo ine?” (Yes. 44:8) Conco tili ndi udindo woyankha funsoli. Mwa mawu komanso zocita zathu, timapeleka umboni wakuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. Dzina lake ndi lokwezeka kuposa lina lililonse. Ngakhale Satana atiyese motani, timasonyeza kuti timam’kondadi Yehova komanso kuti ndife okhulupilika kwa iye. Mwa njila imeneyi, timakhala ndi mwayi wothandiza kuyeletsa dzina lake.

12. Kodi ulosi wa pa Yesaya 40:​3, 5 unakwanilitsidwa motani?

12 Tikamakhalila kumbuyo dzina la Yehova, kapena kuti mbili yake, timatengela Yesu Khristu. Yesaya ananenelatu za kalambula bwalo amene anali ‘kudzakonza njila ya Yehova.’ (Yes. 40:3) Kodi zimenezi zinakwanilitsidwa motani? Yohane M’batizi anakonzela njila Yesu amene anabwela m’dzina la Yehova ndi kulankhula m’dzina la Yehova. (Mat. 3:3; Maliko 1:​2-4; Luka 3:​3-6) Ulosi umenewu unatinso: “Ulemelelo wa Yehova udzaonekela.” (Yes. 40:5) Kodi ulosi umenewu unakwanilitsidwa bwanji? Yesu atabwela padziko lapansi, anaimilako Yehova m’njila yabwino koposa moti zinali ngati Yehova iyemwini ndiye anabwela padziko lapansi.​—Yoh. 12:45.

13. Kodi tingatengele motani citsanzo ca Yesu?

13 Monga analili Yesu, ifenso ndife mboni za Yehova. Timadziwika ndi dzina la Yehova ndipo timauza munthu aliyense amene takumana naye zocita za Yehova zocititsa cidwi zimene Yehova anacita. Komabe kuti ticite zimenezi, tiyenela kudziwikitsa udindo wofunika wa Yesu poyeletsa dzina la Yehova. (Mac. 1:8) Yesu ndiye Mboni ya Yehova yopambana onse ndipo timatengela citsanzo cake. (Chiv. 1:5) Koma kodi dzina la Yehova liyenela kukhala lofunika motani kwa aliyense wa ife?

MMENE TIMAONETSELA KUTI DZINA LA YEHOVA N’LOFUNIKA KWA IFE

14. Malinga ndi Salimo 105:​3, kodi timamva bwanji ponena za dzina la Mulungu?

14 Timalinyadila dzina la Yehova. (Welengani Salimo 105:3.) Yehova amasangalala kwambili tikamadzitama mwa iye. (Yer. 9:​23, 24; 1 Akor. 1:31; 2 Akor. 10:17) “Kudzitama mwa Yehova” kutanthauza kunyadila kuti Yehova ndi Mulungu wathu. Timauona kuti ndi mwayi wapadela kulemekeza dzina lake ndi kukweza mbili yake. Sitiyenela kucita manyazi kuuza anzathu akunchito, anzathu akusukulu, maneba athu, komanso anthu ena kuti ndife Mboni za Yehova. Mdyelekezi amafuna kuti tisamauzeko ena za Yehova. (Yer. 11:21; Chiv. 12:17) Ndipo Satana ndi aneneli ake abodza amafuna kuti anthu aiwale dzina la Yehova. (Yer. 23:​26, 27) Koma cikondi cathu pa dzina la Yehova cimatipangitsa kukhala osangalala “tsiku lonse” cifukwa ca dzinalo.​—Sal. 5:11; 89:16.

15. Kodi kuitanila pa dzina la Yehova kumatanthauza ciyani?

15 Timapitiliza kuitanila pa dzina la Yehova. (Yow. 2:32; Aroma 10:​13, 14) Kuitanila pa dzina la Yehova sinkhani yongodziwa dzina la Mulungu ndi kuligwilitsa nchito. Kumaphatikizapo kudziwa umunthu wa Mulungu, kumukhulupilila, komanso kuyang’ana kwa iye kuti atithandize ndi kutitsogolela. (Sal. 20:7; 99:6; 116:4; 145:18) Timalengezanso dzina lake ndi makhalidwe ake kwa ena ndipo timawalimbikitsa kuti alape ndi kucitapo kanthu kuti Yehova awayanje.​—Yes. 12:4; Mac. 2:​21, 38.

16. Kodi tingaonetse bwanji kuti Satana ndi wabodza?

16 Ndife okonzeka kuvutika cifukwa ca dzina la Yehova. (Yak. 5:​10, 11) Tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova tikamavutika, timaonetsa poyela kuti Satana ndi wabodza. M’nthawi ya Yobu, Satana ananeneza atumiki onse a Yehova kuti: “Munthu angapeleke ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Satana anali kunena kuti anthu amatumikila Yehova kokha zinthu zikakhala bwino. Koma akakumana ndi zovuta angasiye kum’tumikila. Yobu anaonetsa kuti mfundoyi ndi yabodza mwa kukhalabe wokhulupilika. Mofananamo, ifenso tili ndi mwayi woonetsa kuti sitingafulatile Yehova mosasamala kanthu za kukula kwa mavuto amene Satana angatigwetsele. Tisakaikile ngakhale pang’ono kuti Yehova adzapitiliza kutiyang’anila cifukwa ca dzina lake.​—Yoh. 17:11.

17. Malinga ndi 1 Petulo 2:​12, kodi tingapeleke ulemelelo ku dzina la Yehova m’njila ina iti?

17 Timaonetsa kuti timalilemekeza dzina la Yehova. (Miy. 30:9; Yer. 7:​8-11) Cifukwa cakuti timaimila dzina la Yehova komanso kudziwika ndi dzinalo, zocita zathu zingacititse kuti anthu alilemekeze dzinalo kapena kulinyoza. (Welengani 1 Petulo 2:12.) Conco timafuna kucita zonse zimene tingathe kuti zokamba komanso zocita zathu zipeleke citamando kwa Yehova. Tikatelo, ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, zocita zathu zingapeleke ulemelelo ku dzina la Yehova.

18. Ndi njila ina iti tingaonetsele kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwa ife? (Onaninso mawu am’munsi.)

18 Timaona kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambili kuposa lathu. (Sal. 138:2) N’cifukwa ciyani izi n’zofunika kwambili? Cifukwa nthawi zambili tikamakweza dzina la Yehova, anthu angamadane nafe ndipo angamatikambile zoipa.a Yesu anali wokonzeka kufa imfa yocititsa manyazi komanso ngati cigawenga kuti alemekeze dzina la Yehova. “Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila,” kutanthauza kuti sanaganizile kwambili kuti anthu akumuona motani. (Aheb. 12:​2-4) Iye anaika maganizo ake onse pa kucita cifunilo ca Mulungu.​—Mat. 26:39.

19. Kodi mumaliona motani dzina la Yehova? Nanga n’cifukwa ciyani?

19 Timalinyadila dzina la Yehova ndipo timauona kukhala mwayi kuchedwa Mboni za Yehova. Cifukwa cakuti dzina la Yehova ndi lofunika kwa ife, tidzapitilizabe kum’tamanda ngakhale ena atatinyoza. Dzina la Yehova ndi lofunika kwambili kwa ife kuposa ngakhale dzina lathu limene. Conco tiyeni titsimikize mtima kupitiliza kutamanda Yehova mosasamala kanthu za zovuta zimene Satana angatibweletsele. Mwa kutelo, tidzaonetsa kuti dzina la Yehova ndi lofunika koposa kwa ife monga mmene lilili kwa Yesu Khristu.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’ciyani cimaonetsa kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwa otsatila a Yesu?

  • Ndi nkhani yakukhoti iti imene tilimo?

  • Tingaonetse motani kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwa ife?

NYIMBO 10 Tamandani Yehova, Mulungu Wathu!

a Ngakhale munthu wokhulupilika Yobu anayamba kuganizila dzina lake, kapena kuti mbili yake, mopitilila malile anzake atatu atamuneneza kuti anacita colakwa. Poyamba, pamene iye anataikilidwa ana ake ndi katundu wake wonse, “Yobu sanacimwe kapena kuimba Mulungu mlandu woti wacita zinthu zoipa.” (Yobu 1:22; 2:10) Komabe, pamene anamuimba mlandu wakuti anacita zinazake zoipa, anayamba kulankhula “mosaganiza bwino.” Iye anaika kwambili maganizo ake pa kuteteza dzina lake m’malo moyeletsa dzina la Mulungu, kapena kuti mbili yake.​—Yobu 6:3; 13:​4, 5; 32:2; 34:5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani