NKHANI YOPHUNZILA 14
NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵila Pathu
“Sankhani . . . Amene Mukufuna Kum’tumikila”
“Ine ndi banja langa tizitumikila Yehova.”—YOS. 24:15.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Kutikumbutsa zifukwa zimene tinasankhila kutumikila Yehova.
1. Tiyenela kucita ciyani kuti tikhale ndi cimwemwe ceniceni? Ndipo cifukwa ciyani? (Yesaya 48:17, 18)
ATATE wathu wakumwamba amatikonda kwambili, ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi umoyo palipano komanso m’tsogolo. (Mlal. 3:12, 13) Iye anatilenga ndi maluso apadela, koma sanatipatse mphamvu zodzilamulila tokha kapena mphamvu zodziikila muyeso wa cabwino ndi coipa. (Mlal. 8:9; Yer. 10:23) Iye amadziwa kuti tingakhale ndi cimwemwe ceniceni tikamam’tumikila komanso tikamatsatila malamulo ake.—Welengani Yesaya 48:17, 18.
2. Kodi Satana amafuna kuti tizikhulupilila ciyani? Nanga kodi Yehova wacita ciyani potsutsa bodza limenelo?
2 Satana amafuna kuti tizikhulupilila kuti tingakhale acimwemwe popanda malamulo a Yehova, komanso kuti tingakwanitse kudzilamulila tekha. (Gen. 3:4, 5) Pofuna kuonetsa kuti Satana ndi wabodza, Yehova walola anthu kudzilamulila kwa kanthawi. Sitifunika kucita kupita kutali kuti tione kuti anthu alephela kudzilamulila. Kumbali ina, Malemba ndi odzala ndi zitsanzo za amuna ndi akazi amene anakhala ndi umoyo wokhutilitsa cifukwa cotumikila Yehova. Pa onsewo, munthu amene anapeza cimwemwe copambana ndi Yesu Khristu. Koma coyamba, tiyeni tione zimene zinamupangitsa kusankha kutumikila Yehova. Kenako tione cifukwa cake Atate wathu wakumwamba ndi woyenela kumulambila. Ndipo pamapeto pake, tione zina mwa zifukwa zimene zimatipangitsa kusankha kutumikila Yehova.
CIFUKWA CAKE YESU ANASANKHA KUTUMIKILA YEHOVA
3. Kodi Satana anauza Yesu kuti adzamupatsa ciyani? Nanga kodi Yesu anapanga cisankho cotani?
3 Yesu ali pa dziko lapansi anafunika kusankha kuti adzatumikila ndani. Iye atangobatizika, Satana anamuuza kuti adzamupatsa maufumu onse apadziko lapansi akangomulambila kamodzi kokha. Yesu anamuyankha kuti: “Coka Satana! Cifukwa Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” (Mat. 4:8-10) N’cifukwa ciyani Yesu anapanga cisankhoco? Tiyeni tione.
4-5. Ndi zifukwa zina ziti zinapangitsa Yesu kusankha kutumikila Yehova?
4 Cikondi ndico cifukwa cacikulu cinapangitsa Yesu kusankha kutumikila Yehova. Yesu ali ndi cikondi cacikulu komanso cosasunthika pa Atate wake. (Yoh. 14:31) Kuwonjezela apo, Yesu amatumikila Yehova cifukwa ndico cinthu coyenela kucita. (Yoh. 8:28, 29; Chiv. 4:11) Yesu adziwa kuti Yehova ndiye Kasupe wa moyo, ndi wodalilika, komanso kuti ndi wowolowa manja. (Sal. 33:4; 36:9; Yak. 1:17) Nthawi zonse Yehova anali kuphunzitsa Yesu coonadi, ndipo anamupatsa zonse zimene anali nazo. (Yoh. 1:14) Koma mosiyana ndi Yehova, Satana ndiye anacititsa kuti anthufe tizifa. Iye ndi wabodza, ndipo zocita zake zimasonkhezeledwa ndi dyela komanso kudzikonda. (Yoh. 8:44) Podziwa mfundo zimenezi, Yesu sanaganizilepo ngakhale pang’ono kutengela Satana mwa kupandukila Yehova.—Afil. 2:5-8.
5 Cifukwa cina cinapangitsa Yesu kusankha kutumikila Yehova n’cakuti anali kuona zotsatilapo zabwino zimene zinali kudzakhalapo cifukwa cotumikila Yehova mokhulupilika. (Aheb. 12:2) Anadziwa kuti akakhalabe wokhulupilika adzayeletsa dzina la Atate wake, ndipo adzapeleka njila yothetsela mavuto amene Mdyelekezi anayambitsa.
CIFUKWA CAKE YEHOVA NDIYE WOYENELA KUMULAMBILA
6-7. N’cifukwa ciyani ambili masiku ano satumikila Yehova? Nanga ndi cifukwa ciyani Iye ndi woyenela kumulambila?
6 Ambili masiku ano satumikila Yehova cifukwa sadziwa makhalidwe ake ocititsa cidwi, ndipo sadziwa zonse zimene iye waacitila. Ndi mmenenso zinalili ndi anthu amene mtumwi Paulo anawalalikila mumzinda wa Atene.—Mac. 17:19, 20, 30, 34.
7 Paulo anafotokozela anthu a ku Atenewo kuti Mulungu woona ndiye “amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zinthu zonse.” Anakambanso kuti: “Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” Mulungu ndiye Mlengi, amene “kucokela mwa munthu mmodzi anapanga mitundu yonse ya anthu.” Conco cifukwa ca zimenezi, iye ndi woyenela kumulambila.—Mac. 17:25, 26, 28.
8. N’ciyani cimene Yehova sangacite? Fotokozani.
8 Popeza Yehova ndiye Mlengi komanso Ambuye Wamkulu Koposa m’cilengedwe conse, akanafuna akanakakamiza anthu kuti azimutumikila. Koma Yehova sangacite zimenezo. M’malomwake, anatipatsa umboni woonetsa kuti iye aliko, komanso wakuti amatikonda aliyense wa ife payekhapayekha. Amafuna kuti anthu oculuka zedi akhale mabwenzi ake kwamuyaya. (1 Tim. 2:3, 4) Kuti zimenezi zitheke, Yehova watiphunzitsa mmene tingaphunzitsile ena colinga cake, ndi kuwauzako zinthu zabwino zimene adzacitila mtundu wa anthu. (Mat. 10:11-13; 28:19, 20) Watiika mu mpingo ndipo watipatsanso oyang’anila acikondi kuti azitisamalila.—Mac. 20:28.
9. Kodi cikondi ca Yehova cimaonekela motani?
9 Cikondi capadela ca Yehova cimaonekela ndi mmene amacitila ndi anthu amene amanyalanyaza mfundo yakuti iye aliko. Ganizilani izi: M’mbili yonse ya anthu, anthu mabiliyoni asankha kuyendela mfundo zawo pa nkhani ya cabwino ndi coipa. Ngakhale n’telo, Yehova mokoma mtima waapatsa zimene akufunikila kuti akhalebe ndi moyo komanso kuti azisangalala nawo. (Mat. 5:44, 45; Mac. 14:16, 17) Iye waapatsa mwayi wosangalala ndi ubale wacikondi, kulela ana, komanso kusangalala ndi madalitso amene amabwela cifukwa cogwila nchito molimbika. (Sal. 127:3; Mlal. 2:24) Izi zionetsa kuti Atate wathu wakumwamba amakonda aliyense. (Eks. 34:6) Tiyeni tsopano tikumbutsane zina mwa zifukwa zimene zimatipangitsa kusankha kutumikila Yehova komanso mmene amatidalitsila tikatelo.
CIFUKWA CAKE TIMASANKHA KUTUMIKILA YEHOVA
10. (a) Kodi cifukwa cacikulu cimene timatumikilila Yehova n’citi? (Mateyo 22:37) (b) Kodi Yehova wakulezelani mtima motani? (Salimo 103:13, 14)
10 Monga mmene zinalili ndi Yesu, nafenso timatumikila Yehova cifukwa comukonda kwambili. (Welengani Mateyo 22:37.) Timasonkhezeledwa kumukonda Yehova tikaphunzila za makhalidwe ake. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova walezela nafe mtima. Aisiraeli atam’pandukila, iye anawacondelela kuti: “Conde, bwelelani nʼkusiya njila zanu zoipa.” (Yer. 18:11) Yehova amakumbukila kuti ndife opanda ungwilo, ndife fumbi. (Welengani Salimo 103:13, 14.) Mukasinkhasinkha za kuleza mtima kwa Yehova komanso makhalidwe ake ena abwino ocititsa cidwi, kodi samakusonkhezelani kufuna kumutumikila kwamuyaya?
11. Ndi zifukwa zina ziti zimene zimatipangitsa kusankha kutumikila Atate wathu wakumwamba?
11 Cifukwa cina cotipangitsa kutumikila Yehova n’cakuti ndico cinthu coyenela kucita. (Mat. 4:10) Cina, tidziwa zabwino zimene zidzatulukapo tikatumikila Yehova mokhulupilika. Tikakhala okhulupilika, timathandizila kuyeletsa dzina la Yehova, kuonetsa kuti Mdyelekezi ndi wabodza, ndiponso timakondweletsa mtima wa Atate wathu. Tikasankha kutumikila Yehova palipano, tidzakhala ndi ciyembekezo comutumikila kwamuyaya!—Yoh. 17:3.
12-13. Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Jane ndi Pam?
12 Tikali acicepele, tingakulitse cikondi cathu pa Yehova cimene cidzapitiliza kuyaka pamene tikukula. Onani zinacitikila atsikana awili apacibale, Jane ndi Pam.a Jane anali ndi zaka 11, ndipo Pam anali ndi zaka 10 pomwe anayamba kuphunzila Baibulo. Ngakhale kuti makolo awo sanali kufuna kuphunzila Baibulo, analola ana awo kuti azigwilizana ndi Mboni malinga ngati anawo angamapite ku chalichi ndi makolowo kumapeto kwa mlungu. Jane anati. “Zimene ndinaphunzila kwa Mboni kucokela m’Baibulo, zinandithandiza kukaniza cikakamizo ca anzanga cakuti ndigwilitseko nchito amkola bongo komanso kucitako ciwelewele.”
13 Patapita zaka zingapo, onse awili anakhala ofalitsa. Kenako anayamba upainiya kwinaku akusamalila makolo awo okalamba. Pokumbukila zimene zinawacitikila, Jane anati: “Ndinadzionela ndekha kuti Yehova amasamalila mokhulupilika mabwenzi ake monga ikambila 2 Timoteyo 2:19 kuti, ‘Yehova amadziwa anthu ake.’” Mosakaikila, Yehova amasamala za anthu amene amamukonda ndi kumutumikila!
14. Kodi tingayeletse motani dzina la Yehova m’mawu komanso zocita zathu? (Onaninso zithunzi.)
14 Timafuna kuyeletsa dzina la Yehova ku zitonzo zonse zimene Satana wabweletsa pa dzinalo. Tinene kuti muli ndi bwenzi la pamtima lomwe ndi lopatsa, lokhululuka, komanso lokoma mtima. Ndiye tsiku lina mukumva wina akunena kuti mnzanuyo ndi wankhanza komanso wacinyengo. Kodi mungatani? Mungalikhalile kumbuyo bwenzi lanulo. Mofananamo, Satana komanso amene ali kumbali yake akafuna kuipitsa mbili ya Yehova mwa kufalitsa mabodza ponena za Iye, timamukhalila kumbuyo Yehova pouzako ena coonadi. (Sal. 34:1; Yes. 43:10) Timaonetsa kuti tifuna kutumikila Yehova ndi moyo wathu wonse m’mawu komanso zocita zathu.
Kodi mudzalikhalila kumbuyo dzina la Yehova? (Onani ndime 14)b
15. Kodi mtumwi Paulo anapindula motani atasintha zinthu pa umoyo wake? (Afilipi 3:7, 8)
15 Timakhala okonzeka kusintha zinthu pa umoyo wathu kuti titumikile Yehova movomelezeka kapena mokulilapo. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anasankha kusiya udindo wolemekezeka umene anali nawo m’Ciyuda kuti atsatile Khristu ndi kutumikila Yehova. (Agal. 1:14) Zotsatilapo zake n’zakuti anakhala ndi umoyo wokhutilitsa, ndipo analandila mwayi wokalamulila ndi Khristu kumwamba. Iye sanadziimbepo mlandu pa cisankho cimene anapanga cotumikila Yehova. Ifenso sitidzatelo.—Welengani Afilipi 3:7, 8.
16. Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Julia? (Onaninso zithunzi.)
16 Tikakhazikitsa maganizo athu pa kutumikila Yehova, tidzakhala ndi moyo wokhutilitsa palipano komanso m’tsogolo. Onani zinacitikila mlongo wina dzina lake Julia. Asanaphunzile coonadi, Julia anali wa khwaya m’chalichi mwawo kungoyambila ali wacicepele. Katswili wina woimba anaona luso lake ndipo anayamba kumuphunzitsa. Posapita nthawi Julia anachuka ndipo anali kuimba mu malo omveka. Akuphunzila za nyimbo pa sukulu yodziwika kwambili, mnzake wina wa m’kalasi anayamba kukamba naye za Mulungu, ndipo anamufotokozela kuti Mulungu ali ndi dzina lakuti Yehova. Posakhalitsa, Julia anayamba kuphunzila Baibulo kawili pa mlungu. Pamapeto pake, iye anasankha kugwilitsa nchito moyo wake kutumikila Yehova m’malo mokhala woimba wochuka. Sizinali zapafupi kupanga cisankho cimeneci. Iye anakamba kuti, “Ambili anali kundiuza kuti sindinaganize bwino poleka kuimba kuti nditumikile Yehova, koma ndinali kufuna kutumikila Yehova ndi mtima wanga wonse.” Kodi iye amamva bwanji akaganizila cisankho cimene anapanga zaka 30 zapitazo? Iye anati, “Ndili ndi mtendele wa mumtima, ndipo ndili ndi cidalilo cakuti Yehova adzakwanilitsa zokhumba zonse za mtima wanga m’tsogolo.”—Sal. 145:16.
Tikakhazikitsa maganizo athu pa kutumikila Yehova, tidzakhala ndi umoyo wokhutilitsa kwambili (Onani ndime 16)c
PITILIZANI KUTUMIKILA YEHOVA
17. Kodi mfundo yakuti tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiliza, ikuwakhudza bwanji amene akutumikila Mulungu komanso amene akalibe kuyamba kutelo?
17 Tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiliza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “‘Kwatsala kanthawi kocepa’ ndipo ‘amene akubwelayo afika ndithu, sacedwa.’” (Aheb. 10:37) Kodi izi zikutikhudza bwanji? Nthawi imene yatsalako kuti anthu asankhe kutumikila Yehova yafupika. (1 Akor. 7:29) Ndipo ngati tinapanga kale cisankho cotumikila Mulungu, tidziwa kuti ngakhale kuti tiyenela kupilila mavuto, ndi kwa “kanthawi kocepa.”
18. Kodi Yesu ndi Yehova akufuna kuti tizicita ciyani?
18 Yesu sanangolimbikitsa ophunzila ake kuti ayambe kumutsatila, koma kuti azimutsatila mosalekeza. (Mat. 16:24) Conco ngati takhala tikutumikila Yehova kwa nthawi yaitali, tiyeni titsimikize mtima kuti tisaleke. Tiyeni ticite camuna kuti tisaleke kumutumikila. N’zoona kuti kucita zimenezi kungakhale kovuta. Koma tidzakhala acimwemwe, ndipo tidzalandila madalitso ambili ngakhale palipano!—Sal. 35:27.
19. Kodi tikuphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Gene?
19 Ena amaganiza kuti kutumikila Yehova kumamanitsa zambili zabwino. Ngati ndinu wacicepele, kodi ndi mmene mumaonela? M’bale wina wacinyamata dzina lake Gene anati: “Ndinali kuganiza kuti kukhala wa Mboni za Yehova kumamanitsa zambili. Zinali kuoneka ngati acicepele amene ndinali kukula nawo anali kusangalala ndi zinthu ngati kupita ku maphwando, kukhala ndi zibwenzi, kusewela magemu aciwawa pa kompyuta, koma ine ndinali kungokhalila kupita ku misonkhano ndi mu utumiki.” Kodi kuganiza conco kunamukhudza bwanji Gene? Iye anati, “Ndinayamba kukhala umoyo wapawili, ndipo kwa kanthawi zinali kundisangalatsa. Koma izi sizinandibweletsele cimwemwe cokhalitsa. Ndinayamba kuganizila mfundo za m’Baibulo za coonadi zomwe ndinali nditazinyalanyaza, ndipo ndinapanga cisankho cotumikila Yehova ndi mtima wonse. Ndipo kucokela nthawiyo, ndakhala ndikuona kuti Yehova wakhala akuyankha lililonse la mapemphelo anga.”
20. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciyani?
20 Wamasalimo anaimbila Yehova kuti: “Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha nʼkumubweletsa pafupi ndi inu, kuti akhale mʼmabwalo anu.” (Sal. 65:4) Tiyeni titsimikize mtima kutengela citsanzo ca Yoswa yemwe anati: “Ine ndi banja langa tizitumikila Yehova.”—Yos. 24:15.
NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova
a Maina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mayi akuona anthu otsutsa akucita cionetselo kunja kwa malo a msonkhano. Iye akuyandikila kasitandi ka mabuku ndipo akumva mawu a coonadi.
c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Cithunzi coyelekezela cisankho cimene Julia anapanga kuti agwilitse nchito moyo wake kutumikila Yehova.