N’cifukwa Ciani Mulungu Amatilimbikitsa Kupemphela?
Mulungu amatipempha kuti tikhale naye paubwenzi.
Anthu amene ali pa ubwenzi amalankhulana nthawi zonse kuti alimbitse ubwenzi wao. N’cimodzimodzinso ndi Mulungu, iye amatipempha kuti tizikamba naye n’colinga cakuti tikhale naye paubwenzi wabwino. Iye amati: “Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndidzakumvetselani.” (Yeremiya 29:12) Ngati mumakamba ndi Mulungu, ‘mumamuyandikila ndipo iyenso amayandikila kwa inu.’ (Yakobo 4:8) Baibulo limatitsimikizila kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.” (Salimo 145:18) Conco, nthawi zonse tikamapemphela, ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba kwambili.
“Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.”—Salimo 145:18
Mulungu amafuna kukuthandizani.
Yesu anati: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? Cotelo ngati inuyo, . . . mumadziŵa kupeleka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!” (Mateyu 7:9-11) Zoonadi, Mulungu akukupemphani kupemphela kwa iye cifukwa “amakudelani nkhawa” ndipo amafuna kukuthandizani. (1 Petulo 5:7) Iye akukupemphaninso kuti muzimuuza mavuto anu. Baibulo limatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.
Anthu amafunika zinthu za kuuzimu.
Akatswili oona pa zaumoyo wa anthu, apeza kuti anthu mamililiyoni amaona kuti kupemphela n’kofunika. Ngakhale anthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu, naonso amaona kufunika kopemphela.a Zimenezi zingoonetsa kuti anthu analengedwa kuti azikonda zinthu za kuuzimu. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu.” (Mateyu 5:3) Conco, njila yabwino yokhutilitsila zosoŵa zimenezo ndi kukambilana ndi Mulungu nthawi zonse.
Tingapindule bwanji ngati tivomeleza ciitano ca Mulungu cakuti tizipemphela kwa iye?
a Mu 2012, bungwe lofufuza nkhani la Pew Research Center, linapeza kuti ku United States, 11 pelesenti ya anthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu, amapemphela kamodzi pa mwezi.