LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 December masa. 3-7
  • Kukhala “Zinthu Zonse Kwa Anthu Osiyana-siyana”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukhala “Zinthu Zonse Kwa Anthu Osiyana-siyana”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUYAMBA KUTUMIKILA YEHOVA
  • KUTUMIKILA M’DZIKO LACILENDO
  • MAUDINDO AMENE ANAFUNA KUTI NIPITILIZE KUSINTHA
  • NIKALI KUWONGOLELA MBALI ZINA
  • N’nasiya Zinthu Zina Pofuna Kutsatila Ambuye
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Nakhala Nikusangalala Kuphunzila za Yehova na Kuphunzitsako Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Tinaona Cisomo ca Mulungu m’Njila Zambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 December masa. 3-7

MBILI YANGA

Kukhala “Zinthu Zonse Kwa Anthu Osiyana-siyana”

Yosimbiwa na Denton Hopkinson

Denton Hopkinson pamene anali wacicepele

“Ukakabatizika cabe, ndiye kudzakhala kutha kwa cikwati na ine!” Munali mu 1941 pamene atate anaopseza amayi na mau amenewa. Koma amayi sanaope. Iwo anasankha kubatizika kuonetsa kudzipeleka kwawo kwa Yehova Mulungu. Monga mwa mau awo, atate anacoka pakhomo. Panthawiyo n’nali na zaka 8 cabe.

PAMENE izi zinali kucitika, n’nali n’takhala kale na cidwi ndi coonadi ca m’Baibo. Amayi anali atapezako zofalitsa zophunzilila Baibo, ndipo n’nali kukonda kuziŵelenga, makamaka kuonamo mapikica. Atate anali kuletsa amayi kuniuzako zimene anali kuphunzila. Koma popeza n’nali na cidwi, n’nali kufunsa mafunso. Conco anali kuphunzila nane atate akacokapo. Pa cifukwa cimeneci, inenso n’nafuna kudzipeleka kwa Yehova. Mu 1943, n’nabatizika mu mzinda wa Blackpool, ku England. Apo n’nali na zaka 10.

KUYAMBA KUTUMIKILA YEHOVA

Kuyambila nthawi imeneyo, ine na amayi tinayamba kuyendela pamodzi mu ulaliki nthawi zonse. Pokambilana uthenga wa m’Baibo na munthu, tinali kuseŵenzetsa magilamafoni. Anali aakulu ndi olemela makilogilamu 4.5. Tangoganizilani nili wam’ng’ono n’tanyamula cigilamafoni!

N’tafika zaka 14, n’nali kufuna kuyamba upainiya. Ndiye amayi ananiuza kuti nikakambe na mtumiki woyendela (amene lomba timati woyang’anila dela). Iye ananilangiza kuti niphunzileko luso linalake limene lidzanithandiza pocita upainiya. Ndipo n’zimenedi n’nacita. N’tagwila nchito kwa zaka ziŵili, n’nafunsanso woyang’anila dela wina za upainiya. Ananiuza kuti, “Kulekelanji!”

Conco, mu April 1949, ine na amayi tinagulitsa katundu wathu amene tinali naye m’nyumba ya lendi, ndipo wina tinapatsa anthu ena. Tinasamukila ku Middleton, pafupi na mzinda wa Manchester, kumene tinayamba upainiya wathu. Patapita miyezi inayi, n’nasankha m’bale wina kukhala mnzanga wocita naye upainiya. Ofesi ya nthambi inatipempha kusamukila ku mpingo watsopano ku Irlam. Amayi nawo ndi mlongo wina anakacitila upainiya ku mpingo wina.

Olo kuti n’nali na zaka 17 cabe, anatipatsa udindo pamodzi na mnzanga wocititsa misonkhano. Zinali conco cifukwa abale apaudindo anali ocepa mumpingo watsopanowo. Patapita nthawi, ananipempha kusamukila ku Mpingo wa Buxton umene unali na ofalitsa ocepa ndipo unafunikila thandizo. Nimaona kuti zonsezo zinali kunikonzekeletsa maudindo a kutsogolo.

Denton Hopkinson pamodzi ndi ena aitainila anthu ku nkhani ya anthu onse mu 1953

Apo tikumemeza nkhani ya anthu onse pamodzi na ena m’tauni ya Rochester, ku New York, mu 1953

Mu 1951, n’nalemba fomu yofunsila Sukulu ya Giliyadi. Komabe, mu December 1952, boma linaniitana kuti niloŵe usilikali. N’napempha kuti anipatule papulogilamuyo pamaziko akuti n’nali mtumiki wa nthawi zonse, koma khoti inakana pempho langa. Conco, inagamula kuti nikapike jele kwa miyezi 6. Nili m’ndendemo, n’nalandila ciitano ca sukulu ya Giliyadi ya namba 22. Conco, mu July 1953, n’nakwela boti yochedwa Georgic kuyenda ku New York, ku America.

Pamene n’nafika, n’napezekapo pa msonkhano wakuti Dziko Latsopano wa mu 1953. Ndiyeno n’nakwela sitima yopita ku South Lansing ku New York, kumene kunali sukuluyo. Pokhala wongocotsedwa kumene m’ndende, n’nali n’kandalama kocepa. N’taseluka sitima, n’nakwela basi yonipeleka ku South Lansing. Ndalama yolipilila n’nacita kukongola kwa winawake amene n’nakwela naye basi.

KUTUMIKILA M’DZIKO LACILENDO

Sukulu ya Giliyadi inatiphunzitsa zinthu zambili zotithandiza ‘kukhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.’ (1 Akor. 9:22) Tonse atatu—Ine, Paul Bruun, na Raymond Leach—anatitumiza ku Philippines. Tinayembekeza kwa miyezi ingapo kuti maviza athu acoke. Ndiyeno, tinauyamba ulendo wa panyanja kupitila ku Rotterdam, ku nyanja ya Mediterranean, ya Suez, ya Indian, ku Malaysia, mpaka ku Hong Kong. Masiku 47 tili panyanja! Potsiliza, tinafika mumzinda wa Manila pa 19 November, 1954.

Denton Hopkinson na Raymond Leach ali m’boti mu 1954

Ine na mmishonale mnzanga Raymond Leach tinayenda masiku 47 pa boti kupita ku Philippines

Ndiyeno tinafunikila kuzoloŵela anthu atsopano, dziko latsopano, ndi kuphunzila cinenelo catsopano. Koma poyamba, tonse atatu anatiika ku mpingo wina m’tauni ya Quezon, mmene anthu ambili anali kukamba Cizungu. Cifukwa ca ici, pa miyezi 6, tinali tinangophunzila mau ocepa cabe m’Citagalogi. Komabe, asainimenti yotsatila inathetsa vuto limeneli.

Tsiku lina, mu May 1955 titafika panyumba kucokela mu utumiki, ine na M’bale Leach tinapeza makalata m’cipinda cathu. Makalatawo anali otidziŵitsa kuti tinaikidwa kukhala oyang’anila dela. N’nali na zaka 22 cabe, koma udindowu unanipatsa mwayi ‘wokhala zinthu zonse kwa anthu osiyana-siyana’ m’njila zatsopano.

Denton Hopkinson akamba nkhani ya anthu onse

Apo nikamba nkhani ya poyela m’Cibiko pa msonkhano wadela

Mwacitsanzo, n’nakamba nkhani yoyamba ya anthu onse monga woyang’anila wadela pamtetete patsogolo pa shopu ya m’mudzimo. N’nazindikila kuti cinali cikhalidwe cawo ku Philippines, kuti nkhani ya anthu onse izikambidwadi poyela. Pocezela mipingo yosiyana-siyana m’dela, n’nali kupeleka nkhani m’tumakhumbi twaudzu, m’mitsika, pamabwalo a maholo a khanso, pamabwalo a maseŵela, m’mapaki, ndipo nthawi zambili m’makwalala. Tsiku lina, mumzinda wa San Pablo munagwa cimvula camphamvu cakuti n’nalephela kukamba nkhani ya poyela m’maliketi. Conco n’napempha abale audindo kuti nikakambile nkhaniyo m’Nyumba ya Ufumu. Pambuyo pake, abalewo ananifunsa ngati nkhaniyo angailembe pa lipoti monga nkhani ya anthu onse popeza siinakambidwile poyela.

Tinali kukhala m’nyumba za abale. Ngakhale kuti nyumbazo sizinali zapamwamba, zinali zaudongo nthawi zonse. N’nali kugona pa mphasa. Bafa yosambila sinali kanyumba kochingika bwino ayi. Conco, n’naphunzila kusamba mosamala m’kamsasa kapanja. N’nali kukwela tumamotoka na mabasi. Nthawi zina n’nali kukwela boti poyenda ku zisumbu zina. Nthawi yonse imene natumikila, sin’nakhalepo na motoka yanga-yanga.

Kulalikila na kucezela mipingo kunan’thandiza kuphunzila kukamba Citagalogi. Sin’naloŵepo sukulu yophunzitsa cinenelo cimeneci. N’nangociphunzila mwa kumvetsela abale akamalalikila na pamisonkhano. Abale anali ofunitsitsa kunithandiza kuti niphunzile, ndipo nimawayamikila cifukwa ca kuleza mtima kwawo na kuniwongolela moona mtima.

M’kupita kwa nthawi, maudindo ena atsopano anan’thandiza kusinthanso m’mbali zina. Mu 1956 pamene M’bale Nathan Knorr anaticezela, n’napatsidwa nchito yothandiza anthu pa msonkhano waukulu m’dzikolo. Kanali koyamba kugwilako nchitoyo, koma abale anadzipeleka kuti anithandize. Caka cisanathe, kunakonzedwanso msonkhano wina, ndipo M’bale Frederick Franz wocokela ku likulu anaticezela. Potumikila monga woyang’anila msonkhano wacigawo, n’naona kuti m’bale Franz analidi wofunitsitsa kucita zinthu poganizila cikhalidwe ca anthu. Zimenezi zinanicititsa cidwi. Abale a kumeneko anakondwela kwambili kuona M’bale Franz atavala covala ca Cifilipino cochedwa barong Tagalog pokamba nkhani.

Pamene n’naikidwa kukhala woyang’anila cigawo, n’nafunikanso kupanga masinthidwe ena. Panthawiyo, tinali kutambitsa kanema yacizungu yakuti The Happiness of the New World Society. Nthawi zambili tinali kuitambitsila panja kumalo opezeka anthu oculuka. Nthawi zina tinali kulumiwa na tudoyo. Tunali kutsatila laiti ya pulojekita, cakuti mpaka tunali kuloŵa mkati mwa pulojekita. Pambuyo pake, tinali kukhala na nchito yoyeletsa pulojekita. Sicinali copepuka kukonzekela na kutambitsa makanema amenewa. Koma tinali kukondwela tikaona mmene anthu anali ofunitsitsa kulidziŵa bwino gulu la Yehova.

Azibusa a Cikatolika anali kuletsa olamulila kuti asatipatse cilolezo cocita misonkhano yathu. Nthawi zina anali kuyesa kusokoneza mapulogilamu athu mwa kuliza mabelo a chechi yawo akationa tikucita misonkhano kufupi nawo. Koma tinapitiliza nchito yathu, moti anthu ambili a kumeneko ni alambili a Yehova tsopano.

MAUDINDO AMENE ANAFUNA KUTI NIPITILIZE KUSINTHA

Mu 1959, n’nalandila kalata yonidziŵitsa kuti n’naitanidwa kukatumikila pa ofesi ya nthambi. Izi zinacititsa kuti niphunzilenso zinthu zina zambili. M’kupita kwa nthawi, anayamba kunitumiza kukayendela nthambi za ku maiko ena. Pa ulendo wina, n’nadziŵana ndi mlongo Janet Dumond, mmishonale wa ku Thailand. Tinalembelana makalata kwa kanthawi ndithu, ndipo pothela pake tinamanga banja. Tatumikila pamodzi mosangalala monga banja kwa zaka 51.

Denton na Janet Hopkinson ku Philippines

Nili na Janet pa cisumbu cina ku Philippines

Mu umoyo wanga wonse, nakhala na mwayi woyendela anthu a Yehova m’maiko 33. Ndine woyamikila maningi kuti maudindo anga oyambilila ananikonzekeletsa mmene ningathetsele zopinga zimene zimakhalapo cifukwa cocita zinthu na anthu ambili. Maulendo amenewa anan’thandiza kupitiliza kuona zinthu moyenela. Anan’thandizanso kuona mmene Yehova amakondela anthu a mitundu yonse.—Mac. 10:34, 35.

Denton na Janet Hopkinson alalikila mzimayi

Timayesetsa kutengako mbali mu ulaliki nthawi zonse

NIKALI KUWONGOLELA MBALI ZINA

N’zokondweletsa kwambili kutumikila pamodzi na abale athu ku Philippines. Pali pano, ciŵelengelo ca ofalitsa caŵilikiza ka 10 kuposa mmene cinalili n’tangofika m’dzikoli. Ine na Janet tikupitiliza kutumikila pa ofesi ya nthambi ya ku Philippines mumzinda wa Quezon. Natumikila m’dziko lacilendoli kwa zaka zoposa 60. Koma ndine wokonzekanso kusintha malinga na zimene Yehova anganipemphe kucita. Masinthidwe amene acitika m’gulu posacedwapa atiphunzitsa kukhala okonzeka kusintha pamene titumikila Mulungu na abale athu.

Denton na Janet Hopkinson akamba na kamtsikana ka Mboni

Timakondwela tikaona ciŵelengelo ca Mboni cikuwonjezeka

Tayesetsa kucita zonse zimene tinali kuona kuti ni cifunilo ca Yehova, ndipo umenewu wakhala umoyo wokhutilitsa. Kuwonjezela apo, tapanga masinthidwe ofunikila kuti titumikile abale athu. Inde, ndife otsimikiza mtima, malinga ngati Yehova alola, kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyana-siyana.”

Denton Hopkinson akamba na m’bale wacinyamata pa Beteli ku Philippines

Tikali kutumikila pa ofesi ya nthambi ku Quezon City

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani