Gwilitsilani Nchito Tumapepala twa Uthenga Kufalitsa Uthenga Wabwino
1. Kodi tumapepala twa uthenga twagwilitsilidwa nchito bwanji ndi anthu a Mulungu?
1 Tumapepala twa uthenga wa m’Baibo, kapena kuti mathilakiti, twakhala tukugwilitsilidwa nchito ndi atumiki a Yehova kwa nthawi yaitali. Mu 1880, C. T. Russell ndi anzake anayamba kusindikiza Tumapepala twa Uthenga twa Ophunzila Baibo. Ndipo tumapepalato tunali kupatsidwa kwa amene anali kuŵelenga Nsanja ya Olonda kuti azitugaŵila kwa anthu ena. Tunali tofunika kwambili. Conco mu 1884, pamene C. T. Russell analembetsa Bungwe lao lalamulo losacita malonda, n’colinga cakuti apititse patsogolo nchito ya Ufumu, liu la kuti “thilakiti,” analiphatikiza pa dzina lakuti Zion’s Watch Tower Tract Society. Bungweli masiku ano limachedwa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Pofika m’caka ca 1918, Ophunzila Baibo anafalitsa tumapepala toposa 300 miliyoni. Mpaka masiku ano tumapepalato tukali cida cothandiza polalikila.
2. N’cifukwa ninji tumapepala twa uthenga n’tothandiza?
2 Cimene Tulili Tothandiza: Tumapepala twa uthenga n’tokopa kwambili. Uthenga wake wacidule ndi wogwila mtima ndi wothandiza. Tumakopa cidwi ca eninyumba amene angagwe ulesi kuŵelenga magazini athu kapena buku. Tumapepalatu n’tosavuta kugaŵila. Ngakhale ofalitsa atsopano, ndi ana omwe angatugaŵile mosavuta. N’tosavutanso kunyamula.
3. Fotokozani cocitika canu ca muulaliki, kapena cofalitsidwa, coonetsa mmene tumapepala twa uthenga tumathandizila.
3 Anthu ambili anayamba kuphunzila coonadi cifukwa ca kapepala ka uthenga. Mwacitsanzo, mai wina ku Haiti anaona kapepala kathu pamseu. Atakatola n’kukaŵelenga, anati “Ndapeza coonadi!” M’kupita kwa nthawi, anapita ku Nyumba ya Ufumu, n’kuyamba kuphunzila Baibo, pambuyo pake anabatizika. Izi zinatheka cifukwa ca mphamvu ya Mau a Mulungu a m’kapepala ka uthenga.
4. Ngati cogaŵila ca mwezi ndi tumapepala twa uthenga, kodi colinga cathu ciyenela kukhala ciani?
4 Kunyumba ndi nyumba: Popeza kuti tumapepala twa uthenga ndi cida cothandiza polalikila, tudzayamba kukhala cogaŵila ca mwezi nthawi ndi nthawi, kuyambila mwezi wa November. Colinga cathu sikungolandilitsa tumapepalato kwa eninyumba ai, koma kuyambitsa makambilano. Ngati tapeza munthu wacidwi paulendo woyamba kapena wobwelelako, tingaonetse munthuyo mmene timacitila phunzilo la Baibo pogwilitsila nchito buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa, kapena cofalitsa cina cophunzitsila Baibo. Nanga tingagaŵile bwanji tumapepalato kunyumba ndi nyumba? Kapepala kalikonse n’kosiyana. Conco, tiziŵelenga coyamba ndi kutumvetsetsa tumapepala tumene tifuna kugaŵila.
5. Kodi tingagaŵile bwanji tumapepala twa uthenga kunyumba ndi nyumba?
5 Tizigwilizanitsa ulaliki wathu ndi gawo lathu, komanso ndi kapepala komwe tikugaŵila. Tingayambe ulaliki wathu mwa kupatsa mwininyumba kapepala ka uthenga. Maonekedwe ake okongola angakope cidwi ca munthuyo. Kapenanso tingamuonetse tumapepala tungapo kuti asankhepo kamene wakonda. Polalikila m’gawo limene anthu sakonda kutuluka tikagogoda, tinganyamule kapepalako ndi kuonetsa mwininyumba kumaso kwake kwa kapepalako. Kapena tingam’pemphe ngati tingakakankhile munsi mwa citseko ndi kuti atiuze maganizo ake pa zimene aŵelenge. Ngati mutu wa kapepalako ndi funso, tingapemphe mwininyumba kuti akambepo maganizo ake. Mwina tingam’funse funso logwilizana ndi kapepalako, limene lingadzutse cidwi kuti tiyambe makambilano. Ndiyeno tingaŵelenge naye mbali ina ya kapepalako, tikumaima pamafunso amene alimo ndi kum’pempha kukambapo. Tiŵelenge m’Baibo malemba ofunika kwambili. Titakambilana ndime zina, tingamalize makambilano athu ndi kupangana naye za ulendo wobwelelako. Ngati m’dela lanu n’kololeka kusiya mabuku pamakomo pomwe palibe athu, mungasiye kapepala ka uthenga pamalo amene sikangaonekele kwa anthu ena.
6. Kodi tumapepala twa uthenga tingatugwilitsile nchito bwanji muulaliki wa mumseu?
6 Ulaliki wa Mumseu: Kodi munagwilitsilapo nchito tumapepala twa uthenga muulaliki wa mumseu? Anthu ena oyenda mumseu amakhala ofulumila moti kumakhala kovuta kuti aime ndi kukambilana nafe. Kungakhale kovuta kudziŵa cidwi ceni-ceni ca anthu otelowo. Conco, m’malo mowapatsa magazini atsopano amene mwina sadzawaŵelenga n’komwe, bwanji osawapatsa cabe kapepala? Popeza kamakhala ndi maonekedwe okopa, ndipo uthenga wake ndi wacidule, anthu angakhale ofunitsitsa kukaŵelenga akapeza mpata pang’ono. Koma ngati sali ofulumila, tingakambilane nao mfundo zina za m’kapepalako.
7. Fotokozani zocitika muulaliki zoonetsa mmene tingagwilitsilile nchito tumapepala twa uthenga polalikila mwamwai.
7 Ulaliki Wamwai: Kulalikila mwamwai ndi tumapepala twa uthenga n’kosavuta. M’bale wina amanyamulako twina m’thumba akamacoka panyumba. Akakumana ndi munthu, monga wogulitsa m’sitolo, amam’pempha kuti am’patseko kanthu kena koŵelenga, basi n’kum’patsa kapepala ka uthenga. Pamene munthu wina ndi mkazi wake anali kukonza ulendo wopita ku mzinda kukaona malo, anazindikila kuti kumeneko adzakumana ndi anthu ocokela ku maiko osiyana-siyana. Conco, anatenga kabuku kakuti Mitundu Yonse ndi tumapepala twa uthenga twa zinenelo zosiyana-siyana. Ali kumeneko, amati akamva munthu akulankhula cinenelo cina amene akugulitsa zinthu m’mbali mwa mseu, kapena amene wakhala naye pafupi pamalo ocezela kapena pamalo odyela, anali kum’gaŵila kapepala ka uthenga m’cinenelo cake.
8. Kodi tumapepala twa uthenga tuli ngati mbeu m’njila yanji?
8 “Bzala Mbeu Zako”: Tumapepala twa uthenga tingatuyelekezele ndi mbeu. Mlimi amamwaza mbeu zake paliponse m’munda mwake. Amatelo cifukwa sadziŵa kuti n’ziti zidzamela. Mlaliki 11:6 amati: “Bzala mbeu zako m’maŵa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, cifukwa sukudziŵa pamene padzacite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzacite bwino.” Conco, tiyeni tipitilize kufalitsa cidziŵitso mwa kugwilitsila nchito cida cimeneci cothandiza kwambili.—Miy. 15:7.
[Mau okopa papeji 3]
Popeza kuti tumapepala twa uthenga n’tothandiza kwambili polalikila, nthawi ndi nthawi kuyambila mwezi wa November, tudzakhala cogaŵila ca mwezi