Ndandanda ya Mlungu wa October 15
MLUNGU WA OCTOBER 15
Nyimbo 101 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 13 ndime 17-24 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Danieli 10-12 (Mph. 10)
Na. 1: Danieli 11:15-27 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cake Akristu Sabwezela Coipa—Aroma 12:18-21 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Atumiki a Mulungu Okhulupilika Amapezeka M’machalichi Osiyana-siyana Acikristu?—rs tsa. 142 ndime 3-5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 106
Mph. 10: Ngati munthu anena kuti, ‘Sindifuna.’ Kukambilana kozikidwa pa buku la Kukambitsilana, tsamba 16, ndime 1, mpaka tsamba 18, ndime 1. Kambilanani mayankhidwe ena amene alembedwa m’bukumo, ndiponso ena amene agwilitsilidwapo nchito mogwila mtima m’gawo la kwanuko. Citani zitsanzo ziŵili zoonetsa mmene tingayankhile.
Mph. 20: “Gwilitsilani Nchito Tumapepala twa Uthenga Kufalitsa Uthenga Wabwino.” Mafunso ndi Mayankho. Pokambilana ndime 5, fotokozani mwacidule tumapepala twa uthenga togaŵila m’mwezi wa November, ndipo citani citsanzo cogaŵila kapepala kamodzi. Pokambilana ndime 7, khalani ndi citsanzo cogwilitsila nchito tumapepala twa uthenga muulaliki wamwai.
Nyimbo 97 ndi Pemphelo