Kodi Mukhoza Kumacitako Ulaliki wa M’madzulo?
1. Malinga ndi buku la katswili wina, kodi mtumwi Paulo anali kukonda kulalikila nthawi yanji ku nyumba ndi nyumba?
1 Buku la katswili wina lofotokoza zaumoyo wa anthu ochulidwa m’Baibo (Daily Life in Bible Times) limati, mtumwi Paulo anali kulalikila nyumba ndi nyumba “kuyambila 16 hrs mpaka usiku kwambili.” Sitidziŵa ngati imeneyi ndiyo nthawi yeni-yeni imene Paulo anali kulalikila nthawi zonse. Cimene tidziŵa n’cakuti anali wofunitsitsa ‘kucita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino.’ (1 Akorinto 9:19-23) Ayenela kuti anali kulinganiza bwino zocita zake kuti azitha kulalikila ku nyumba ndi nyumba panthawi imene akanatha kulankhula ndi anthu ambili.
2. N’cifukwa ninji m’madzulo ndi nthawi yabwino yolalikila?
2 M’madela ambili, ofalitsa amakonda kulalikila ku nyumba ndi nyumba nthawi zam’maŵa mkati mwa mlungu. Koma kodi imeneyi ndiyo nthawi yabwino kudela lanu? Tamvelani zimene mpainiya wina anafotokoza ponena za gawo lake. Iye anati: “N’kovuta kupeza anthu panyumba nthawi ya masana. Ambili amapezeka m’madzulo.” Ulaliki wa m’madzulo ungakhale mwai wabwino wolalikila kwa amuna. Panthawi imeneyi, eninyumba amakhala omasukilapo ndiponso osavuta kweni-kweni kulankhulana nao. Ngati kungakhale kothandiza kumakumana m’madzulo kaamba ka ulaliki, akulu angalinganize zimenezo.
3. Kodi tingakhale bwanji ozindikila pamene tikucita ulaliki wa m’madzulo?
3 Khalani Wozindikila: Pamene tili muulaliki wa m’madzulo m’pofunika kukhala wozindikila. Mwacitsanzo, mukafika pakhomo la munthu pa nthawi yosayenelela, monga panthawi ya cakudya, ndi bwino kufunsa ngati mungabwelenso panthawi ina. Ngati ndi usiku, imani pamalo amene mwininyumba angakuoneni bwino, ndipo mudzidziŵikitse msanga ndi kunena cimene mwabwelela. Ndi bwinonso kukhala aŵili aŵili kapena m’tumagulu ndi kuyenda mumseu umene uli ndi malaiti owala bwino. Musamafike pakhomo la munthu usiku kwambili pamene akukonzekela kukagona. (2 Akor. 6:3) Ngati kumaloko n’koopsa usiku, muzilalikila m’madzulo kusanade.—Miy. 22:3.
4. Kodi ulaliki wa m’madzulo uli ndi mapindu anji?
4 Mapindu Ake: Ulaliki umakoma pamene tipeza anthu olankhula nao. Ngati tilalikila kwa anthu oculuka, timakhala ndi mwai wothandiza anthu ambili kuti ‘adziŵe coonadi molondola kuti akapulumuke.’ (1 Tim. 2:3, 4) Kodi mungathe kulinganiza bwino zocita zanu kuti muzicita nao ulaliki wa m’madzulo?