LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 4/15 tsa. 1
  • Muzigwilitsila Nchito Bwino Nthawi Yanu mu Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzigwilitsila Nchito Bwino Nthawi Yanu mu Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mumakwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Mukhoza Kumacitako Ulaliki wa M’madzulo?
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 4/15 tsa. 1

Muzigwilitsila Nchito Bwino Nthawi Yanu mu Ulaliki

Mboni za Yehova zinathela maola 1,945,487,604 mu ulaliki m’caka ca utumiki ca 2014. Umenewu ndi umboni wakuti ndife otsimikiza kukhala otangwanika mu utumiki wa Yehova. (Sal. 110:3; 1 Akor. 15:58) Popeza kuti “nthawi yotsalayi yafupika,” tiyenela kuyesetsa kugwilitsila nchito nthawi imene ndi yamtengo wapatali kufikila anthu ambili mu ulaliki.—1 Akor. 7:29.

Kuti tigwilitsile nchito bwino nthawi yathu mu ulaliki tiyenela kukhala okonzeka kusintha. Mwacitsanzo, kodi mungasinthe ndandanda yanu n’colinga cakuti mukambe ndi anthu ambili ngati mwaona kuti mwakhala ola limodzi kapena kuposelapo musanakambe ndi munthu pocita ulaliki winawake? Zocitika zimasiyanasiyana malinga ndi malo. Komabe, mfundo zotsatilazi zingakuthandizeni kuti mugwilitsile nchito bwino nthawi yanu kuti mupewe ‘kumenya mphepo.’—1 Akor. 9:26.

  • Ulaliki wa Kunyumba ndi Nyumba: Kwa zaka zambili, ofalitsa akhala akuyamba ulaliki wao mwa kupita kunyumba ndi nyumba. Koma popeza kuti anthu ambili amagwila nchito, kodi simungasinthe pulogalamu yanu yoloŵa mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, kuti mucite ulalikiwo madzulo pamene anthu ambili ali panyumba ndipo akupumula? Kucita ulaliki wa mumseu kapena wa pamalo amalonda masana kungakhale ndi zotsatilapo zabwino.

  • Ulaliki Wapoyela: Mathebulo ndi mashelufu amawilo ayenela kuikidwa pa malo amene pamadutsa anthu ambili m’gawo la mpingo wanu. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2013 tsa. 5.) Ngati anthu ambili aleka kudutsa pamalo amene tinasankha kucitilapo ulaliki wapoyela, Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingasankhe kuti shelufu yamawilo kapena thebulo ziikidwe pamalo ena pamene pamadutsa anthu ambili.

  • Maulendo Obwelelako ndi Maphunzilo a Baibulo: Ngati mwaona kuti maulaliki ena sayenda bwino panthawi inayake, kodi mungacite maulendo obwelelako ndi kucititsa maphunzilo a Baibulo panthawiyo? Mwacitsanzo, ngati ulaliki wa kunyumba ndi nyumba umayenda bwino pa Ciŵelu m’maŵa, mungakonze zotsogoza phunzilo la Baibulo masana kapena madzulo.

N’zoona kuti timaŵelenga nthawi imene timathela mu ulaliki, komabe, timakondwela kwambili ngati ulaliki wathu umakhala ndi zotsatilapo zabwino. Ngati mwaona kuti kucita ulaliki winawake sikuyenda bwino pa nthawi inayake, mungacite bwino kuyesa ulaliki wina. Pemphelani kwa Yehova, “mwini zokolola,” kuti akutsogoleleni kugwilitsila nchito bwino nthawi yanu mu ulaliki.—Mat. 9:38.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani