Maulaliki Acitsanzo
Mmene Tingagawile Kapepala Koitanila Anthu Ku Cikumbutso
“Tabwela pano kuti tikupatseni kapepalaka kokuitanilani ku cocitika cofunika kwambili pa caka cimene cidzakhalako pa 26 March. Ili ndi tsiku lokumbukila imfa ya Yesu. Kudzakhala nkhani imene idzafotokoza mmene timapindulila ndi imfa yake ndipo idzakhala ya mahala. Kapepalaka kaonetsa nthawi ndi malo kumene tidzacitila mwambo umenewu m’dela lathu lino.”
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova March 1
“Anthu ena afunsapo funso ili, ‘Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu anaukitsidwadi? Kodi inu munayamba mwadzifunsapo funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Onani cifukwa cake funso limenelo ndi lofunika kwambil. [Ŵelengani 1 Akorinto 15:14.] Magazini iyi ifotokoza mmene timadziwila kuti ciukililo ca Yesu si nkambakamwa cabe.”
Galamukani! March
“Kodi muvomeleza kuti ino ndi nthawi yovuta kulela ana? [Yembekezani ayankhe.] Makolo ambili apeza malangizo othandiza m’Baibo. Mwacitsanzo, lembali lakhala likuthandiza azibambo kupeza mipata yoyamikila ana ao ndi kuwalimbikitsa. [Ŵelengani Akolose 3:21.] Magazini iyi ili ndi mfundo zisanu zimene zingathandize azibambo kuyamikila ndi kulimbikitsa ana ao.”