Danga la Mafunso
◼ Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibo zimene zionetsa mmene tiyenela kugwilitsila nchito mafoni pa misonkhano ndi muulaliki?
“Ciliconse cili ndi nthawi yake.” (Mlal. 3:1): Mafoni amapatsa anthu mwai wakuti azilembelana mameseji kapena kukambilana nthawi iliyonse. Komabe, pali nthawi zina pamene Akristu samafuna kudodometsedwa ndi mafoni ao. Mwacitsanzo, nthawi ya misonkhano ndi nthawi yolambila Yehova, yolandila malangizo a kuuzimu, ndi kulimbikitsana. (Deut. 31:12; Sal. 22:22; Aroma 1:11, 12) Zingakhale bwino kuzima foni yathu tikafika pamisonkhano ndi kuona mameseji pambuyo pake. Ngati tikuyembekezela zina zimene zingafune kuti tisazime foni yathu, tiyenela kuiseting’a m’njila yakuti isasokoneze ena.
‘Citani Zinthu Zonse Cifukwa ca Uthenga Wabwino.’ (1 Akor. 9: 23): Nthawi zina, pamakhala zifukwa zabwino zogwilitsila nchito foni muulaliki. Mwacitsanzo, m’bale amene atsogolela angagwilitsile nchito foni kudziŵa kumene ena akulalikila m’gawo. Nthawi zina, ofalitsa angagwilitsile nchito foni kutumila munthu wacidwi kapena phunzilo la Baibo asanapite kwa munthuyo, maka-maka ngati munthuyo akhala kutali kwambili. Ngati tili ndi foni, tiyenela kusamala kuti isatisokoneze pamene tikambilana ndi mwininyumba. (2 Akor. 6:3) Poyembekezela ofalitsa ena, cingakhale bwino kuika maganizo athu pa ulaliki ndi anthu amene tilalikila nao, m’malo motumila mnzathu foni kapena meseji.
Muziganizila Ena. (1 Akor. 10:24; Afil. 2:4): Sitiyenela kucedwela dala kufika pa kukumana kokonzekela ulaliki, n’colinga cakuti tidzatumila wina wake foni kapena meseji kuti tidziŵe kumene kagulu kakulalikila. Tikafika mocedwa, tidzacititsa kuti woyang’anila kagulu asinthe anthu amene agaŵidwa kale. N’zoona kuti zocitika za mwadzidzidzi zimatipangitsa kuti nthawi zina tizicedwa. Komabe, cikakhala cizoloŵezi cathu kufika mwamsanga, tidzaonetsa kuti timalemekeza makonzedwe a Yehova, m’bale amene akutsogolela, ndi ofalitsa anzathu.