“Sindimupezanso Panyumba!”
Kodi munalankhulapo mau amenewa ponena za munthu amene anaonetsa cidwi? Kuthilila mbeu ya coonadi imene munafesa kumakhala kovuta ngati munthuyo simum’peza. (1 Akor. 3:6) Nthawi zina, ofalitsa ozoloŵela ulaliki amalembela kalata munthu amene samupeza panyumba kapena amamulembela kapepala n’kukasiya munsi mwa citseko. Ofalitsa ena akaona kuti zidzakhala zovuta kupezanso munthuyo panyumba, amam’pempha nambala ya foni. Mungalembe ulendo wobweleza pamene mwafikila munthu amene munalalikila, kaya mocita kumulembela kalata, imelo, uthenga pafoni, kumulembela kapepala kapena kumutumila foni. Kucita zimenezi kungakulitse cidwi ca munthuyo ngakhale kuti sapezekapezeka panyumba.