UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu ambili amene amacita cidwi na uthenga wa ufumu, amafuna-funa coonadi pa za Mulungu. (Yes. 55:6) Kuti tiwaphunzitse mofikapo, tifunika kupitako mobweleza-bweleza. Anthu amakumana na zovuta zosiyana-siyana, conco, njila imene tingakulitsile cidwi cawo siingafanane. Komabe, kuti tikhale aluso tifunika kukonzekela bwino na kukhala na colinga pa ulendo uliwonse. Colinga cathu cacikulu ni kuyambitsa phunzilo la Baibo.
MMENE TINGACITILE:
Yesetsani kubwelelako mwamsanga, mwina m’masiku ocepa cabe.—Mat. 13:19
Khalani waubwenzi ndi waulemu. Khalani womasuka
Yambani mwa kuwapatsa moni waubwenzi. Muzichula dzina lawo. Akumbutseni cimene mwabwelela—kaya n’kudzayankha funso, kubweletsa magazini yatsopano, kuŵaonetsa webusaiti, kuŵatambitsa vidiyo, olo kuŵaonetsa mmene timacitila phunzilo la Baibo. Sinthani ulaliki wanu ngati cidwi cake capita pa nkhani ina.—Afil. 2:4
Thililani mbeu ya coonadi imene munabyala mu mtima mwake mwa kukambilana naye mfundo ya m’Malemba, kapena kumusiyila cofalitsa. (1 Akor. 3:6) Yesani kukhazikitsa ubwenzi naye.
Yalani maziko a ulendo wotsatila