CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | AMOSI 1-9
Funani-funani Yehova, Kuti Mukhalebe na Moyo
5:6, 14, 15
Kodi kufuna-funa Yehova kumatanthauza ciani?
Kumatanthauza kupitiliza kuphunzila za Yehova na kukhala mogwilizana na miyezo yake.
N’ciani cinacitikila Aisiraeli atalephela kufuna-funa Yehova?
Analeka ‘kudana ndi coipa na kukonda cabwino’
Anaika maganizo awo pa kudzikondweletsa okha
Ananyalanyaza uphungu wa Yehova
Kodi Yehova watipatsa ciani pofuna kutithandiza kumufuna-funa?