November 6-12
AMOSI 1-9
Nyimbo 60 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Funani-funani Yehova, Kuti Mupitilize Kukhala na Moyo”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Amosi..]
Amosi 5:4, 6—Tifunika kum’dziŵa Yehova na kucita cifunilo cake (w04 11/15 peji 24 pala. 20)
Amosi 5:14, 15—Tifunika kuvomeleza miyezo ya Yehova ya cabwino na coipa na kuikonda (jd peji 90-91 mapa. 16-17)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Amosi 2:12—Kodi tingatsatile bwanji malangizo a pa vesili? (w07 10/1 peji 14 pala. 8)
Amosi 8:1, 2—Kodi “dengu la zipatso za m’cilimwe” liimila ciani? (w07 10/1 peji 14 pala. 6)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Amosi 4:1-13
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani na kukambilana mavidiwo payokha-payokha.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako” (15 min.) Kukambilana. Ndiyeno tambitsani na kukambilana vidiyo yoonetsa ofalitsa aŵili akucita ulendo wobwelelako.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr“Cigawo 7—Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano,” nkhani 21 mapa. 1-7
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 143 na Pemphelo