LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 5/13 tsa. 2
  • Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Kambilanani Nkhani Imodzi, Koma Gaŵilani Magazini Onse Aŵili
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 5/13 tsa. 2

Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?

1. Tikamaŵelenga nkhani zimenezi m’makope athu a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, kodi tiyenela kuganizila ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?

1 Pokonza nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amazikonza molingalila anthu kulikonse padziko lapansi. Ndiye cifukwa cake, nkhani zake zimakhala zosiyana-siyana. Tikamaŵelenga nkhani zimenezi m’makope athu, tiyenela kuganiza kuti ndi anthu otani amene angacite nazo cidwi, kenako, tiyenela kuwagaŵila anthuwo.

2. Kodi ndi nkhani ziti zimene zimapezeka m’magazini athu zimene zingacititse cidwi anthu ena?

2 Kodi Nsanja ya Olonda yaposacedwapa ili ndi nkhani ya m’Baibo imene munakambilanapo ndi anzanu a kunchito? Kapena ili ndi nkhani yonena za umoyo wa banja imene ingathandize wacibale wanu? Kodi pali mnzanu amene akulingalila kupita kudziko lina limene linachulidwa mu Galamukani!? Kodi pali magazini ena amene angasangalatse anthu a zamalonda kapena mabungwe aboma m’gawo lanu? Mwacitsanzo, magazini imene imakamba za mavuto amene acikulile amakumana nao, ingakhale yothandiza maka-maka kwa okhala ku malo osungilako anthu okalamba. Mabungwe oona zamalamulo angasangalale ndi magazini imene ili ndi nkhani yonena za upandu.

3. Fotokozani cocitika coonetsa ubwino wogaŵila anthu magazini amene ali ndi nkhani zimene zigwilizana mwacindunji ndi zocitika paumoyo wao.

3 Zotsatilapo zake: Banja lina ku South Africa litalandila Galamukani! ya October 2011, yamutu wakuti, “Kodi Mungalele Bwanji Ana Anu Kuti Akule Bwino?,” linatumila foni masukulu okwana 25 a m’gawo lao. Aphunzitsi okwana 22 analandila makope amenewa ndi kugaŵila ana a sukulu. Banja lina m’dziko limeneli linacita zofanana ndipo linagaŵila makope a magazini imeneyi ku masukulu a m’dela lao. Aphunzitsi pa sukulu lina anakonza zakuti pofotokoza zolinga za sukulu lao mlungu wina agwilitsile nchito magazini imeneyi ndipo anacitanso zofanana pa pulogalamu yao yoŵelenga. Banja limeneli linauzako woyang’anila dela za cocitika cimeneci, cakuti woyang’anila dela analimbikitsa kuti mipingo izilalikila ku masukulu amene ali m’gawo lao. Ofalitsa ambili anapempha magazini imeneyi ku ofesi ya nthambi, cakuti ofesi ya nthambi inacitanso kusindikiza ena.

4. N’cifukwa ciani tifunika kugaŵila magazini athu kwa anthu ambili?

4 Magazini athu amafotokoza zinthu zimene zimacitika masiku ano ndipo amalimbikitsa anthu kudalila Baibo ndi kuika ciyembekezo cao pa Ufumu wa Mulungu. Magazini amenewa ndi okhawo amene “akulengeza za cipulumutso” padziko lonse lapansi. (Yes. 52:7) Ndiye cifukwa cake, tifunika kuwafalitsa kwa anthu ambili. Njila yabwino yocitila zimenezi ndiyo kudzifunsa kuti ‘Ndani angacite nazo cidwi izi?’

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani