Kambilanani Nkhani Imodzi, Koma Gaŵilani Magazini Onse Aŵili
Magazini athu onse amakhala ndi nkhani zosiyana-siyana komanso zocititsa cidwi. M’malo mokambitsilana nkhani zingapo ndi mwininyumba, ndi bwino kungokambilana nkhani imodzi. Ngati timayang’anitsitsa tikafika pakhomo komanso ngati nkhani zimene zili m’magazini tizidziŵa bwino, tingasankhe nkhani mwina mu Nsanja ya Olonda kapena mu Galamukani! imene ingacititse cidwi mwininyumba. Mwacitsanzo, ngati taona zoseŵeletsa za ana m’nyumba kapena pabwalo, tingasankhe kukambilana ndi mwininyumba nkhani yonena za umoyo wa banja. Ngati tapeza mwamuna panyumba, tingasankhe kukambilana naye nkhani imene imacititsa cidwi amuna, monga boma labwino. Ngakhale kuti tingakambilane cabe nkhani imodzi, tiyenela kugaŵila mwininyumba magazini onse aŵili ngati aonetsa cidwi.