Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Amosi
1. N’cifukwa ciani citsanzo ca Amosi cimatilimbikitsa?
1 Kodi munayamba mwadzionapo kukhala wosayenelela kulalikila cifukwa ndinu wosaphunzila ndi wosauka? Ngati n’conco, mudzalimbikitsidwa ndi citsanzo ca Amosi. Iye anali woweta nkhosa ndiponso mlimi, koma Yehova anam’patsa mphamvu zolengeza uthenga wofunika kwambili. (Amosi 1:1; 7:14, 15) Mofananamo, Yehova amagwilitsila nchito anthu odzicepetsa masiku ano. (1 Akor. 1:27-29) Kodi ndi maphunzilo ena ati amene tingawagwilitsile nchito mu utumiki amene tiphunzila kwa mneneli Amosi?
2. N’cifukwa ciani tiyenela kukhalabe olimba pamene tikumana ndi citsutso mu utumiki?
2 Khalanibe Olimba Pamene Mukumana ndi Citsutso: Pamene Amaziya amene anali wansembe wolambila mwana wa ng’ombe m’ufumu wa Isiraeli wa kumpoto wa mafuko 10 anamva ulosi wa Amosi, iye anayankha kuti: ‘Pita kunyumba! Coka pano! Ife tili kale ndi cipembedzo cathu!’ (Amosi 7:12, 13) Amaziya anapotoza mau a mneneli pamene anali kupempha Mfumu Yerobowamu kuti iletse Amosi kugwila nchito yake. (Amosi 7:7-11) Koma Amosi sanacite mantha. Masiku ano, atsogoleli a cipembedzo ena amafuna andale kuwathandiza pamene akuzunza anthu a Yehova. Komabe, Yehova akutilimbikitsa kuti palibe cida cidzapangidwa kuti cikuvulaze cimene cidzapambana.—Isa. 54:17.
3. Kodi ndi uthenga wa mbali ziŵili uti umene timalengeza masiku ano?
3 Lengezani Ciweluzo ca Mulungu ndi Madalitso Ake a Mtsogolo: Ngakhale kuti Amosi analosela za ciweluzo ca ufumu wa kumphoto wa Isiraeli wa mafuko 10, anamaliza buku la m’Baibo lokhala ndi dzina lake mwa kulemba za lonjezo la Yehova lonena za kubwezeletsa ndiponso madalitso oculuka. (Amosi 9:13-15) Ifenso timalalikila za kubwela kwa “tsiku laciweluzo” la Mulungu koma zimenezi zangokhala cabe mbali ya ‘uthenga wabwino wa ufumu’ umene tiyenela kulengeza. (2 Pet. 3:7; Matt. 24:14) Yehova akadzaononga anthu oipa pa Armagedo njila ya dziko lapansi la paladaiso idzatseguka.—Sal. 37:34.
4. Kodi ndi citsimikizo cotani cimene tili naco cakuti tidzakwanitsa kucita cifunilo ca Yehova?
4 Kulalikila uthenga wa Ufumu m’dziko limene lili ndi anthu ambili otsutsa kumaika paciyeso kutsimikiza mtima kwathu pa kudzipeleka kwa Yehova ndi pocita cifunilo cake. (Yoh. 15:19) Komabe, timadziŵa kuti Yehova adzapitiliza kutipatsa zimene tifunikila kuti ticite cifunilo cake, monga mmene anacitila ndi Amosi.—2 Akor. 3:5.