Bokosi La Mafunso
◼ Kodi mlongo ayenela kuvala cakumutu pamene apita ndi m’bale kuphunzilo la Baibo locititsa coimilila pakhomo?
Ngati mlongo acititsa phunzilo la Baibo lokhazikika ndipo m’bale wobatizika alipo, mlongo ayenela kuvala cakumutu. (1 Akor. 11:3-10) Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, tsamba 27 inafotokoza kuti: ‘Kumeneku n’kuphunzitsa kumene amakhala atakonzelatu ndipo wocititsa phunziloyo amatsogolela ndithu. Pa zocitika ngati zimenezi, phunzilo limenelo limakhala mbali yoonjezela ya maphunzilo a mpingo. Ngati mlongo acititsa phunzilo lotelo ndipo m’bale alipo, mlongo ayenela kuvala cakumutu.’ Mlongo adzafunikanso kuvala cakumutu ngati atsogoza phunzilo pamodzi ndi mwamuna amene ndi wofalitsa wosabatizika. Iye afunika kucita zimenezi kaya atsogozela phunzilo m’nyumba, coimilila pakhomo kapena kwina kulikonse.
Ndipo ngati phunzilo la Baibo locititsa coimilila pakhomo silinakhazikitsidwe, mlongo sangavale cakumutu ngakhale pamene m’bale alipo. Iye sangavale cakumutu ngakhale kuti colinga ca ulendo wobwelelako ndi kusonyeza mocitila phunzilo la Baibo kapena kukambilana nkhani yocokela m’zofalitsa zogwilitsila nchito pophunzitsa. Popeza pamafunika kupanga maulendo obwelelako angapo tisanakhazikitse phunzilo la Baibo locititsa coimilila pakhomo, ofalitsa adzafunika kuona pamene kungakhale koyenela kuvala cakumutu.