UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tizionetsa Ulemu Tikafika pa Khomo la Munthu
Akhristu ali monga “coonetsedwa m’bwalo la maseŵela kudziko.” (1 Akor. 4:9) Conco, sitiyenela kudabwa kuti anthu ena amationela pa windo kapena kumvetsela ali kumbuyo kwa citseko. Pa nyumba zina pangakhale makamela acitetezo kapena maikilofoni yothandiza mwini nyumba kutiona, kutimvetsela, kapena kutijambula mau. Nazi njila zina zotithandiza kuonetsa ulemu tikafika pakhomo la munthu.—2 Akor. 6:3.
ZOCITA ZANU (Afil. 1:27):
Muzilemekeza mwini nyumba mwa kusasuzila kapena kusonjola m’nyumba mwake. Muzipewa kudya, kumwa, kapena kutuma foni na kulemba meseji muli imilile pakhomo la munthu
MAU ANU (Aef. 4:29):
Pamene muli pakhomo la munthu, samalani kuti musakambe zinthu zimene simufuna kuti mwini nyumba amveleko. Pofuna kuika maganizo pa zimene adzakamba, ofalitsa ena amalekeza kukambilana nkhani zawo