LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/13 tsa. 1
  • Mmene Tingakonzekelele Mau Oyamba Ogwila Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingakonzekelele Mau Oyamba Ogwila Mtima
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukonzekela Mau Athu Oyamba
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 12/13 tsa. 1

Mmene Tingakonzekelele Mau Oyamba Ogwila Mtima

1. N’cifukwa ciani kukhala ndi mau oyamba ogwila mtima n’kofunika?

1 Ngati panyumba akukonza cakudya conunkhila bwino, amene akumva fungo la cakudyaco amalaka-laka kuti adyeko. Mofananamo, mau oyamba ogwila mtima amacititsa kuti tikhale ndi makambilano abwino a m’Malemba. Mau oyamba ogwila mtima angasiyane, ena angakhale aatali ena aafupi. Koma mofanana ndi cakudya cokoma, amafunika kuwakonzekela bwino pasadakhale. (Miy. 15:28) Nanga n’ciani cimacititsa mau oyamba kukhala ogwila mtima?

2. Kodi tingakonzekele bwanji mau oyamba okopa cidwi?

2 Sankhani Nkhani Zimene Zingakope Anthu: Mau athu oyamba azikopa anthu, cifukwa kulephela kutelo mwininyumba angathetse makambilanowo. Conco, pokonzekela tiziganizila nkhani zimene zingakope anthu. Kodi anthu a m’dela lathu amafuna boma labwino ndi umoyo wabanja wosangalatsa? Kapena kodi angakonde kuona nkhondo itatha? Nthawi zambili anthu amakonda kupeleka malingalilo ao pankhani imene mukambilana nao, conco konzani funso locititsa munthu kuganiza. Kodi tingagwilitsile nchito citsanzo cimodzi ca mau oyamba ca mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndi kucigwilizanitsa ndi zocitika m’gawo lathu? Nthawi zina zingakhale bwino kuyeseza mau anu oyamba pa Kulambila kwanu kwa Pabanja.

3. Kodi mau athu oyamba tingawagwilizanitse bwanji ndi cikhalidwe ca anthu a m’gawo lathu?

3 Ganizilani Cikhalidwe ca Anthu ndi Kumene Acokela: M’madela ena munthu akafika panyumba, mwamsanga amafunika kukamba cimene wabwelela. Koma ku madela ena, mlendo akafika panyumba ndi kuyamba kulankhula asanafunse umoyo wa mwininyumba kapena kuzidziŵikitsa, kumaoneka kuti ndi kusoŵa ulemu. Pamene kumalo ena, malinga ndi cipembedzo ca anthuwo tikhoza kuyamba makambitsilano athu kucokela m’Baibo. (Mac. 2:14-17) Komabe, ngati anthuwo si Akristu kapena sapita ku cipembedzo ciliconse, zingakhale bwino kuchula nkhani ya m’Baibo paulendo wotsatila.—Mac. 17:22-31.

4. Kodi tiyenela kuganizila ciani pokonza mau athu oyamba?

4 Mau Oyamba: Konzekelani bwino mau anu oyamba. Nthawi zambili mau aafupi ndi osavuta amakhala bwino. N’kofunikanso kuganizila mmene tinganenele mau athu oyamba. Khalani acimwemwe, aubwenzi, ndipo muzionetsa cidwi kwa mwininyumba. Kutsatila malangizo amenewa kudzatithandiza kukonzekela mau oyamba ogwila mtima amene adzalimbikitsa anthu a m’gawo lathu kudya “patebulo la Yehova.”—1 Akor. 10:21.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani