Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukonzekela Mau Athu Oyamba
Cifukwa Cake N’kofunika: Ngati mau athu oyamba si ogwila mtima, mwininyumba angathetse makambilano tisanakamba ulaliki wathu. Conco, ofalitsa ambili amaona kuti mau oyamba ndi mbali yofunika kwambili ya ulaliki wao. Ngakhale kuti tili ndi maulaliki acitsanzo mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndiponso m’buku la Kukambitsirana, si nthawi zonse pamene maulaliki amenewa amakhala ndi mau onse. Izi zili conco n’colinga cakuti tizitha kuwasinthasintha. Ngakhale kuti ulaliki wacitsanzo ungakhale ndi mau onse, ofalitsa angafune kuusintha kapena kukonza ulaliki wao. Conco, tizikhala ogwila mtima ngati tizikonzekela bwino mau athu oyamba m’malo mongokamba zilizonse zimene zabwela m’maganizo pamene mwininyumba atsegula khomo.—Miy. 15:28.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Panthawi ya kulambila kwa pabanja, patulani nthawi yokonzekela ndi kuyeseza mau oyamba.
Mukakhala mu ulaliki, fotokozelani ofalitsa anzanu zimene mwakonzekela kukakamba. (Miy. 27:17) Sinthani mau anu oyamba ngati si ogwila mtima.