Gwilitsilani Nchito “Mfundo za m’Mau a Mulungu”—Poyambitsa Makambilano
1. Ndi cida catsopano citi cimene tingagwilitsile nchito mu ulaliki?
1 Kuciyambi kwa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso kuli mbali yakuti, “Mfundo za m’Mau a Mulungu.” Koma zinenelo zina zili ndi kabuku kamene kali ndi mbali yofanana ndi imeneyi. Kodi kabuku kameneka tingakagwilitsile nchito bwanji pokonzekela maulaliki? Kabukuka ndi kothandiza kwambili poyambitsa makambilano cifukwa kali ndi Malemba angapo munsi mwa funso lililonse mofanana ndi buku la Kukambitsilana.
2. Tingagwilitsile nchito bwanji kabuku kakuti Mfundo za m’Mau a Mulungu mu ulaliki?
2 Ngati mwasankha kugwilitsila nchito funso 8, mungakambe kuti, “Tikukambilana ndi anthu mwacidule funso lakuti ‘kodi Mulungu ndi amene amacititsa kuti anthu azivutika?’ Nanga inuyo muganiza bwanji? [Yembekezani yankho.] Baibulo limapeleka yankho lomveka bwino kwambili pa funso limeneli.” Mwa kugwilitsila nchito Baibulo, ŵelengani ndi kukambilana lemba limodzi kapena angapo amene ndi osagwila mau. Ngati mwininyumba waonetsa cidwi, mungamusonyeze mafunso 20 amene ali kuciyambi kwa kabukuka ndi kumupempha kuti asankhepo funso limene afuna kuti mudzakambilane pa ulendo wotsatila. Kapena mungamupatse cofalitsa cimene timagwilitsila nchito pophunzila Baibulo ndi anthu cimene cili ndi nkhani yogwilizana ndi imene mwakambilana.
3. Kodi kabuku kakuti Mfundo za m’Mau a Mulungu tingakagwilitsile nchito bwanji poyamba kukambilana ndi anthu amene si Akristu?
3 Mungagwilitsile nchito funso 4 ndi 13 mpaka 17 polalikila anthu amene si Akristu. Mwacitsanzo, ngati mwasankha kugwilitsila nchito funso 17 mungakambe kuti: “Lelo tikucezela mabanja mwacidule. Kodi mukuvomeleza kuti mabanja akukumana ndi mavuto ambili lelolino? [Yembekezelani yankho.] Mabanja ambili aona kuti mau anzelu awa akuti: “Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake” ndi othandiza. [Simufunika kuchula kuti mau amenewa acokela pa Aefeso 5:33. Ngati mukulankhula ndi mkazi mungagwile mau a pa Aefeso 5:28.] Kodi muona kuti kugwilitsila nchito malangizo amenewa kungathandize cikwati kuyenda bwino?
4. Kodi mungacite ciani mukamaliza kukambilana ndi munthu amene si wacipembezo cacikristu?
4 Mukamaliza kukambilana, pangani makonzedwe akuti mudzapilize kukambilana pa ulendo wotsatila. Ndiyeno mungasankhe kudzakambilana naye lemba limodzi limene lili munsi mwa funso limene mwagwilitsila nchito. Panthawi ina yoyenela mungamudziŵitse kuti mau anzelu amene mwakhala mukukambilana naye ndi a m’Baibulo. Mogwilizana ndi nkhani zimene munakambilana ndiponso malinga ndi mmene munthuyo amaonela Baibulo Mpatseni cofalitsa cimene muona kuti cingamusangalatse.—Onani nkhani imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu December 2013..