Zaka 100 Zolengeza Ufumu wa Mulungu
1. Kodi anthu a Yehova analimbikitsidwa kucita ciani pafupifupi zaka 100 zapitazo?
1 “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake.” Mau ocititsa cidwi amenewo amene M’bale Rutherford anakamba zaka pafupifupi 100 zapitazo, analimbikitsa kwambili anthu a Yehova kulengeza uthenga wa Ufumu ku madela onse. Ndipo izi n’zimene takhala tikucita. Mofanana ndi Akristu oyambilila, takhala tikulalikila uthenga wabwino wa Ufumu “m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Tikayang’ana m’mbuyo zaka 100 zapitazi, n’ciani cimene takhala tikucita kuti tilengeze Ufumu wa Mulungu? N’ciani cimene cingatithandize kupitiliza kulengeza Ufumuwo pamene ukukwanitsa zaka 100 kucokela pamene unakhazikitsidwa?
2. Kodi zofalitsa zathu zacilikiza bwanji Ufumu wa Mulungu?
2 Kuyang’ana m’Mbuyo: Kwa zaka zambili, zofalitsa zathu zakhala zikucilikiza Ufumu wa Mulungu. Kuyambila mu 1939 magazini yathu imene takhala tikufalitsa kwambili ili ndi mutu wakuti: Nsanja ya Mlonda Imalengeza Ufumu Wa Yehova. Nthawi zambili magaziniyi imafotokoza za Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzacita. Magazini ya Galamukani! imasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiye ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu. Conco n’koyenela kuti magazini aŵiliwa akumasulidwa m’zinenelo zambili komanso kufalitsidwa kwambili padziko lonse lapansi kuposa magazini ena alionse!—Chiv. 14:6.
3. Ndi njila zotani zimene takhala tikugwilitsa nchito kuti tilengeze Ufumu?
3 Anthu a Yehova akhala akugwilitsila nchito njila zosiyanasiyana kuti alengeze Ufumu wa Mulungu. M’nthawi zakale tinali kugwilitsa nchito magalimoto okhala ndi zokuzila mau, mawailesi ndi magalamafoni oyenda nao. Njila zimenezi zinatithandiza kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu ambili panthawi imene kunali olengeza Ufumu ocepa. (Sal. 19:4) M’zaka zaposacedwapa takhala tikulengeza uthenga wa Ufumu kudzela pa jw.org kwa anthu mamiliyoni ambili kuphatikizapo anthu amene amakhala kumadela kumene nchito yathu ndi yoletsedwa.
4. Ndi njila zapadela ziti zimene takhala tikugwilitsila nchito polalikila uthenga wa Ufumu?
4 Anthu a Yehova akhala akugwilitsilanso nchito njila zapadela pofalitsa uthenga wa Ufumu. Mwacitsanzo, kuyambila zaka za m’ma 1990, kuonjezela pa ulaliki wa kunyumba ndi nyumba tinayambanso kulalikila m’mapaki, m’malo oimikamo magalimoto, ndi malo a malonda. Posacedwapa tayamba kucita ulaliki wina wapadela umene ndi ulaliki wapoyela wa m’mizinda ikuluikulu padziko lonse. Kuonjezela pamenepo, mipingo yambili ikucita nao ulaliki wapoyela m’magawo ao pogwilitsa nchito matebulo ndi mashelufu a mawilo okhala ndi mabuku ndi magazini. Amaika mashelufu amenewa ndi matebulo pamalo pamene pamapita anthu ambili. Komabe, ulaliki wa kunyumba ndi nyumba ukali njila yaikulu imene timagwilitsila nchito pa nchito yathu yolalikila uthenga wa Ufumu.—Mac. 20:20.
5. Kodi ambili a ife tidzakhala ndi mipata yotani m’caka ca utumiki catsopano?
5 Nchito ina Mtsogolo: Mu mwezi wa September, tiyamba caka catsopano ca utumiki ndipo anthu ambili adzayamba Upainiya wa nthawi zonse. Kodi inunso mudzayamba upainiya wa nthawi zonse? Ngati n’zovuta kuti muyambe upainiya wanthawi zonse, kodi n’zotheka kuti muzilembetsa upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi? Kaya mudzakwanitsa kuyamba upainiya kapena ai, Yehova adzakudalitsani cifukwa ca kudzimana kwanu potenga nao mbali mokwanila pa nchito yolengeza Ufumu.—Mal. 3:10.
6. N’cifukwa ciani mwezi wa October 2014, udzakhala wapadela?
6 Ufumu wa Mulungu udzakwanitsa zaka 100 mu October 2014, kucokela pamene unabadwa. Mpake kuti mfundo yaikulu ya Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya November–December umenewo ndi yokhudza Ufumu wa Mulungu. Muyenela kucita khama kuti mukafalitse magazini imeneyi kwa anthu ambili. Pamene tikuyembekezela zimene zidzacitika mtsogolo, tiyeni tonse tipitilize “kulengeza uthenga wabwino wonena za ufumu wa Mulungu” kwa anthu onse amene angafune kumva.—Mac. 8:12.