Cida Catsopano Cofufuzila
Ofalitsa mamiliyoni ambili pa dziko lonse lapansi akhala akugwilitsila nchito bwino cida cofufuzila ca Watch Tower Publications Index. Koma cida cimeneci cikupezeka m’zinenelo zocepa cabe cifukwa cili ndi malifalensi ambili amene m’zinenelo zina mulibe. Conco, pakonzedwa Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova limene lamasulidwa m’zinenelo 170. Zofalitsa zimene zinaikidwa m’bukuli ndi zoyambila m’caka ca 2000. Buku Lofufuzila Nkhani limeneli silinasindikizidwe m’zinenelo zimene zili kale ndi buku la Index, koma laikidwa pa CD ya Watchtower Library ndi pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower. Buku Lofufuzila limeneli lidzakuthandizani kufufuza mayankho a mafunso a m’Baibulo ndiponso nkhani zina zimene mufuna. Lidzakuthandizaninso kukonzekela misonkhano ndi kulambila kwa pabanja.