Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda January–February
“Lelo tikupatsa anthu tumapepala twa uthenga utu. Kapepala aka kafotokoza ubwino wogwilitsila nchito malangizo a m’Baibulo. Kapepala kanu ndi aka. [Mpatseni mwininyumba kapepala kakuti Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?] Zioneka kuti m’maboma ziphuphu zakhala vuto la nthawi zonse. Muganiza kuti n’cifukwa ciani zinthu zili conco?[Yembekezelani ayankhe.] Mau awa a m’Baibulo ndi ocititsa cidwi kwambili. [Ŵelengani Mlaliki 7:20.] Magazini iyi ifotokoza cimene Baibulo imanena kuti cidzathetsa ziphuphu. Pezani nthawi yoŵelenga magaziniyi. Tengani yanu iyi.”
Galamukani! February
“Tikugaŵila anzathu magazini yatsopano ya Galamukani! Magaziniyi ikuyankha funso locititsa cidwi kwambili ili. [Aonetseni pacikuto.] Ndingakonde kumva maganizo anu pa citsanzo cili m’magaziniyi. [Ŵelengani Miyambo 29:11.] Kodi muganiza kuti mfundo iyi ndi yothandiza masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ili ndi mfundo zinai za m’Baibulo ndiponso ifotokoza mmene mfundozi zingatithandizile pa umoyo wathu.”