Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda May-June
“Anthu ambili masiku ano sadziŵa kuti Baibulo lili ndi mayankho okhutilitsa a mafunso ngati awa. [Muonetseni mafunso ali kuciyambi kwa nkhani yoyamba m’magazini a Nsanja ya Mlonda ndi kuŵelenga naye 2 Timoteyo 3:16] Magazini iyi ifotokoza mmene mungapezele mayankho m’Baibulo lanu.”
Galamukani! June
“Tonsefe timavutika ndi matenda. Conco tikuceza ndi anzathu mwacidule kuti tikambilane nao vesi lolimbikitsa ili la m’Baibulo. [Ŵelengani Yesaya 33:24a.] Zikanakhala kuti sitidwala, kodi muganiza kuti moyo ukanakhala bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Poyembekezela kuti ulosiwu udzakwanilitsidwe, pali zinthu 5 zimene zingatithandize kukhala ndi thanzi labwino. Magazini iyi ifotokoza zinthu zimenezo.”