LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 7/15 tsa. 2
  • Bokosi La Mafunso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Bokosi La Mafunso
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Mufunika Kubwelelako Mwamsanga
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Colinga ca Webu Saiti Yathu Ndi Kuthandiza Ife ndi Anthu Ena
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 7/15 tsa. 2

Bokosi La Mafunso

◼ Kodi ofalitsa ayenela kugwilitsila nchito kwambili Intaneti kulalikila kapena kuphunzila Baibulo ndi munthu wa kudziko lina?

Ofalitsa ena amagwilitsila nchito intaneti kuti apeze maphunzilo a Baibulo m’maiko amene nchito yathu ndi yoletsedwa kapena mmene ofalitsa ndi ocepa. Nthawi zina, kucita zimenezi kwakhala ndi zotulukapo zabwino. Komabe, pamakhala ngozi ngati ofalitsa amaceza kapena kulankhulana ndi anthu acilendo pa intaneti. Ngakhale kuti intaneti yathandiza anthu amitima yabwino kulandila uthenga wa Ufumu, iyo ingacititse m’bale kapena mlongo kuyanjana ndi anthu oipa ngakhalenso ampatuko. (1 Akor. 1:19-25; Akol. 2:8) Kuonjezela apo, ku maiko amene nchito ya Ufumu ndi yoletsedwa, a boma angaziona mauthenga onse amene mukutumizilana. Zimenezi zingabweletse mavuto kwa abale ndi alongo a m’dzikolo. Conco, ofalitsa sayenela kupita pa intaneti kuti afufuze anthu a kudziko lina kuti awalalikile uthenga wabwino.

Ngati tacita ulaliki wamwai kwa munthu amene wabwela kudzaceza m’dziko lathu, sitiyenela kupitiliza kukulitsa cidwi ca munthuyo akabwelela ku dziko lakwao pokhapo ngati tapatsidwa cilolezo ndi ofesi yathu ya nthambi. M’malo mwake, tingamuonetse mmene angagwilitsile nchito webusaiti ya jw.org, kapena mmene angapezele adilesi ya ofesi ya nthambi ya kwao. Tingamulimbikitsenso kuti akapite ku Nyumba ya Ufumu yakufupi ndi kwao. N’zoona kuti kumaiko ena kulibe Nyumba za Ufumu. Koma, ngati munthuyo afuna kuti Mboni za Yehova zikamufikile, tingadzaze Fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu (S-43) ndi kuipeleka kwa kalembela, amene adzaitumiza ku ofesi ya nthambi pogwilitsila nchito adilesi ya “Mpingo” pa jw.org. Ofesi ya nthambi imene imayang’anila nchito m’dziko limene munthu wacidwiyo akukhala, imadziŵa mmene zinthu zilili m’dzikolo ndipo imakhala pa malo abwino opeleka thandizo la kuuzimu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2014 tsa. 7 ndi wa November 2011 tsa. 2.

Ngati munthu amene tikambilana naye Baibulo anasamukila kudziko lina kapena ngati timaphunzila Baibulo ndi munthu wa kudziko lina amene tinamudziŵa kudzela pa intaneti cabe, ndi bwino kutsatila malangizo amene apelekedwawa. Koma, tingapitilize kukulitsa cidwi ca munthuyo mpaka wofalitsa wa ku dziko lake atapezeka kuti aziphunzila naye Baibulo. Komabe, ngati munthu akhala m’dziko limene nchito yathu ndi yoletsedwa, m’pofunika kukhala osamala kwambili ngati tikukambilana nkhani za m’Baibulo pogwilitsila nchito makalata, mafoni kapena zipangizo zina.—Mat. 10:16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani