CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 45-51
Yehova Sadzanyoza Munthu Wosweka Mtima
Salimo 51 inalembedwa ndi Davide pambuyo pakuti mneneli Natani wamuuza za chimo lalikulu limene anacita ndi Batiseba. Cikumbumtima cinamuvutitsa kwambili Davide, cakuti anavomeleza chimo lakelo modzicepetsa. —2 Sam. 12:1-14.
Davide anacimwa, koma zinali zotheka kulandila thandizo lauzimu
51:3, 4, 8-12, 17
Asanalape ndi kuvomeleza chimo, cikumbumtima cinali kumuvutitsa kwambili
Anavutika kwambili cifukwa cosayanjidwa ndi Mulungu, cakuti anali kudziona ngati munthu amene waphwanyidwa mafupa
Anafunitsitsa kukhululukidwa, kulandila thandizo lauzimu, ndi kukhala ndi cimwemwe cimene anali naco poyamba
Anapempha Yehova modzicepetsa kuti amuthandize kukhala ndi mtima womvela
Anali ndi cidalilo cakuti Yehova adzamukhululukila