CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 7–11
“Mtima Wako Usapatuke”
Mfundo za Yehova za makhalidwe abwino zimatiteteza. Kuti tipindule na mfundo zimenezi, tifunika kuzisunga mumtima mwathu. (Miy. 7:3) Mtumiki wa Yehova akalola mtima wake kupatuka, amakodwa mosavuta ku misampha yokopa ya Satana. Pa Miyambo caputa 7 pamakamba za mnyamata wina amene analola mtima wake kumusoceletsa. Tingaphunzilepo ciani pa zolakwa zake?
Kuona
7:10
Kugwila
7:13
Kulaŵa
7:14
Kumva fungo
7:17
Kumvetsela
7:21
Satana amayesa kuticotsa kwa Yehova mwa kusokoneza maganizo athu kuti atipangitse kucita chimo
Nzelu ndi kudziŵa zinthu zingatithandize kuzindikila mavuto amene tingakumane nawo ngati tacita chimo. Zingatithandizenso kupewa zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu