CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 51-52
Mau Onse a Yehova Amakwanilitsika
Yehova ananenelatu mwatsatane-tsatane zinthu zimene zidzacitika mtsogolo
Msilikali woponya mivi wolondela nyumba ya Mfumu yaciperesiya
“Nolani mivi yanu”
51:11, 28
Amedi ndi Aperisi anali akatswili oponya mivi, ndipo uta ndiwo unali cida cawo codalilika. Anali kunola kwambili mivi yawo kuti akalasa, iziloŵa mozama m’thupi
“Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo”
51:30
Zolemba za Nabonidus Chronicle zimati: “Asilikali a Koresi analoŵa mu Babulo popanda kucita nkhondo.” Izi zigwilizana na ulosi wa Yeremiya
Nabonidus Chronicle
“Babulo adzakhala milu yamiyala [ndiponso] bwinja mpaka kalekale”
51:37, 62
Kuyambila mu 539 B.C.E., ulemelelo wa Babulo unayamba kutha. Alexander Wamkulu anafuna kupanga Babulo kukhala likulu lake, koma anafa mwadzidzidzi. Pamene Cikhristu cinali kuyamba, Ayuda ena anali akali ku Babulo. Ndiye cifukwa cake nthawi zina Petulo anali kupitako. Koma zaka za m’ma 300 C.E., mzindawo unakhala matongwe, ndipo m’kupita kwa nthawi unathelatu