UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulitsani Makhalidwe Aumulungu—Kudzicepetsa
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA:
Kudzicepetsa kumathandiza kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova.—Sal. 138:6
Kudzicepetsa kumathandiza kukhala paubale wabwino na ena.—Afil. 2:3, 4
Kunyada kumawononga.—Miy. 16:18; Ezek. 28:17
MMENE TINGAKULITSILE KUDZICEPETSA:
Pemphani malangizo na kuwaseŵenzetsa.—Sal. 141:5; Miy. 19:20
Muzithandiza ena ngakhale pa nchito zooneka zosika.—Mat. 20:25-27
Musalole kuti maluso kapena maudindo akucititseni kuyamba kudzitukumula.—Aroma 12:3
Ningaonetse bwanji kudzicepetsa mokulilapo?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAKULEPHELETSENI KUKHALA WOKHULUPILIKA —KUDZIKUZA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi zimene timacita tikapatsidwa uphungu zimaonetsa ciani za ise?
Kodi pemphelo limatithandiza bwanji kukulitsa khalidwe la kudzicepetsa?
Tingaonetse bwanji kudzicepetsa?