CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | ZEFANIYA 1-HAGAI 2
Funani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike
Zef. 2:2, 3
Kuti Yehova akatibise pa tsiku la mkwiyo wake, kudzipeleka cabe kwa iye sikokwanila. Tifunikanso kumvela malangizo amene Zefaniya anapeleka kwa Aisiraeli.
Funani Yehova: Limbitsani ubwenzi wanu na Yehova mwa kugwilizana kwambili na gulu lake
Funani cilungamo: Muzitsatila miyezo yolungama ya Yehova
Funani cifatso: Modzicepetsa, muzicita cifunilo ca Mulungu ndi kumalandila uphungu
Ningacite ciani kuti niwonjezele kufuna-funa Yehova, cilungamo cake, na cifatso?