LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 7/14 tsa. 3
  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Zefaniya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Zefaniya
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Funani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
    Phunzitsani Ana Anu
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 7/14 tsa. 3

Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Zefaniya

1. Kodi Zefaniya anatumikila monga mneneli m’njila iti? Nanga iye wakhala bwanji citsanzo cabwino kwa ife lelolino?

1 Kulambila Baala mu Yuda kunali kucitika poyela m’zaka za m’ma 650 B.C.E. Amoni Mfumu yoipa anali ataphedwa ndipo Yosiya Mfumu yacinyamata anali atayamba kulamulila. (2 Mbiri 33:21–34:1) Ndiyeno Yehova anautsa mneneli Zefaniya kuti alengeze uthenga wa Ciweluzo pa nthawi imeneyo. Zefaniya sanacepetse mphamvu ya uthenga umene Yehova anamuuza wonena za kuipa kwa ulamulilo wa Yuda ngakhale kuti iye anali wa m’banja la Cifumu. (Zef. 1:1; 3:1-4) Mofananamo, tifunika kuyesetsa ndithu kutengela citsanzo ca Zefaniya ca kulimba mtima ndi kupewa kulola acibale kutisokoneza pa kulambila kwathu Yehova. (Mat. 10:34-37) Nanga ndi uthenga wotani umene Zefaniya analengeza, ndipo zotsatilapo zake zinali zotani?

2. Tifunika kucita ciani kuti tikabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova?

2 Bwelani kwa Yehova: Ndi Yehova yekha amene angapulumutse anthu pa tsiku la mkwiyo wake. N’cifukwa cake, Zefaniya analimbikitsa anthu a ku Yuda kuti abwele kwa Yehova, ayesetse kukhala olungama ndi kuyesetsa kukhala ofatsa kudakali nthawi. (Zef. 2:2, 3) N’cimodzimodzinso ndi ife masiku ano. Timalimbikitsa ena kubwela kwa Yehova monga mmene Zefaniya anacitila, koma ifenso tifunika kucitapo kanthu, kuyesetsa kusabwelela m’mbuyo pankhani ‘yotsatila Yehova.’ (Zef. 1:6) Motelo kuti tipitilize kutsatila Yehova, tiyenela kuŵelenga Mau ake ndi kupempha citsogozo cake. Timayesetsa kukhala acilungamo mwa kukhala ndi makhalidwe abwino. Timayesetsa kukhala ofatsa mwa kukhala ndi mtima wogonjela ndi kukhala okonzeka kutsogoleledwa ndi gulu la Yehova.

3. N’cifukwa ciani tifunika kukhala ndi maganizo oyenela mu ulaliki?

3 Zotsatilapo Zabwino: Anthu ena m’dziko la Yuda anakhudzidwa ndi uthenga waciweluzo umene Zefaniya anapeleka koma zioneka kuti Yosiya amene anayamba kufunafuna Yehova ali mnyamata ndi amene anakhudzidwa mtima kwambili. Zimenezi zinacititsa Yosiya kuyamba kugwila nchito mwamphamvu pocotsa mafano m’dziko limenelo. (2 Mbiri 34:2-5) Masiku ano, ngakhale kuti mbeu za Ufumu zimagwela m’mbali mwa mseu, pamiyala, kapena pa minga, zina zimagwela pa nthaka yabwino ndi kubala zipatso. (Mat. 13:18-23) Tili ndi cidalilo cakuti Yehova adzapitilizabe kudalitsa khama lathu pamene tili otangwanika kubyala mbeu za Ufumu.—Sal. 126:6.

4. N’cifukwa ciani tiyenela ‘kuyembekezela Yehova’?

4 Anthu ena mu Yuda anaona monga Yehova sangacite ciliconse. Komabe, Yehova anatsimikizila kuti tsiku lalikulu linali kubwela. (Zef. 1:12, 14) Amene anapeza citetezo mwa Iye ndi amene anapulumuka. (Zef. 3:12, 17) Pamene ‘tikuyembekezela Yehova’, tiyeni tipitilizebe kutumikila Mulungu wathu wamkulu mosangalala ndi mogwilizana limodzi ndi alambili anzathu—Zef. 3:8, 9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani