CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 27-28
Pitani Mukapange Ophunzila—Cifukwa ciani, Kuti, ndipo Motani?
Cifukwa ciani? Yesu analandila ulamulilo waukulu kucokela kwa Yehova.
Kuti? Yesu analamula otsatila ake kupanga ophunzila pakati pa “anthu a mitundu yonse”
Kuphunzitsa ena kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamula ni nchito yofunika kupitiliza
Kodi anthu ena tingawaphunzitse bwanji malamulo a Yesu?
Tingawathandize bwanji ophunzila athu kuseŵenzetsa zimene Yesu anaphunzitsa?
Tingawathandize bwanji ophunzila athu kutengela citsanzo ca Yesu?