CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 27–28
Kodi Tingaphunzile Ciani pa Zovala za Ansembe?
28:30, 36, 42, 43
Zovala zimene ansembe aciisiraeli anali kuvala zimatikumbutsa kuti tifunika kufuna-funa citsogozo ca Yehova, kukhala oyela, ndiponso kukhala odzicepetsa komanso aulemu.
Kodi timadziŵa bwanji zimene Yehova afuna kuti ticite?
Kodi kukhala woyela kutanthauza ciani?
Kodi tingaonetse bwanji kudzicepetsa komanso ulemu?