LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 September tsa. 8
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Amene Safuna Kutuluka m’Nyumba

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Amene Safuna Kutuluka m’Nyumba
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Ulaliki Wapoyela M’gawo la Mpingo Wanu
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Tizionetsa Ulemu Tikafika pa Khomo la Munthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Muzionetsa Khalidwe Lopambana mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 September tsa. 8
M’bale na mlongo akufotokoza uthenga wa m’kathilakiti kwa munthu wina pa kamela ili pacitseko.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Amene Sanatuluke m’Nyumba

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Kupita patsongolo kwa sayansi ndiponso kuwonjezeka kwa upandu kwapangitsa kuti makamela akauni-uni komaso ma intakomu akhale ofala m’manyumba. Tingacite mantha pofuna kulalikila munthu amene akutiona koma ife sitikumuona. Malangizo otsatilawa adzatithandiza kuti tisamacite mantha kulalikila pa kamela kapena pa intakomu.

MMENE TINGACITILE:

  • Khalani na maganizo oyenela. Anthu ambili amene ali na makamela kapena ma intakomu m’nyumba zawo amakhala na cifuno cokamba nafe.

  • Kumbukilani kuti makamela akauni-uni ene amayanba kujambula masanalize belo n’komwe pageti, ndipo mwininyumba angakhale kuti wakuonani kale komanso kukumvetselani pamene mwafika pamalopo.

  • Pamene mwininyumba wakuyankani, kambani naye pa intakomu kapena pa kamela monga mmene mungakambilane naye mwacindunji. Muzimwetulila na kucita magesica mwacibadwa. Kambani zimene munakonzekela kummuza mukanaonana naye mwacindunji. Ngati pali kamela, musamaiyandikile pafupi kwambili. Ngati mwininyumba sakuyankha, musasiye uthenga.

  • Pambuyo pakuti makambilano atha, kumbukilani kuti mwininyumbayo angapitilizebe kukuyang’anani na kukumvetselani.

YESANI IZI

M’bale mmodzi-modziyo akuyeseza ulaliki na kudzijambula pa foni yake.

Miziyeseza mwa kudzijambula pa vidiyo ya pa foni yanu mukukamba, ndiyeno tambani mmene mukuonekela.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani