Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao
Cifukwa Cake N’kofunika: Yelekezani kuti mwadziŵa kuti kwatsala pang’ono kuti ngozi yacilengedwe icitike. Ngati anthu sangathamangile kumalo opulumukilako adzafa. Kenako mupita pa nyumba ya munthu woyandikana naye kuti mum’cenjeze, koma iye akuyankhani kuti ndi wotangwanika. Kunena zoona, simungangosiya nthawi imeneyo kumuthandiza. Anthu ambili m’gawo lathu amakana uthenga wathu. Sadziŵa kuti uthenga umene timawapelekela ndi wopulumutsa moyo. Mwina nthawi imene timawacezela io amakhala otangwanika. (Mat. 24:37-39) Kapena mwina amakana cifukwa ca mabodza amene auzidwa. (Mat. 11:18, 19) Iwo angamaone kuti sitisiyana ndi zipembedzo zina zimene zatulutsa zipatso zoipa. (2 Pet. 2:1, 2) Ngati panthawi yoyamba mwininyumba sanaonetse cidwi, tisafulumile kusiya kumulalikila.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Mukacoka panyumba ya munthu amene sanafune kulankhulana naye, muyenela kukambitsilana ndi mnzanu za njila yabwino imene mukanaigwilitsila nchito poyankha mwininyumbayo.