Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Mwininyumba Wokwiya
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Anthu ambili amene timapeza mu ulaliki ndi aulemu. Ngakhale n’conco,Yesu ananenelatu kuti anthu ena adzadana nafe. (Yoh. 17:14) N’cifukwa cake sitiyenela kudabwa ngati tapeza mwininyumba wokwiya. Zimenezi zikacitika, tiyenela kuyankha mwa njila imene imakondweletsa amene timaimila, Yehova. (Aroma 12:17-21; 1 Pet. 3:15) Kucita zimenezi, kudzatithandiza kupewa kukangana ndi mwininyumba. Tidzapelekanso ulaliki wabwino kwa mwininyumba ndi onse oona, ndipo zidzawacititsa kuti akamvetsele ulendo wotsatila Mboni za Yehova zikawayendela.—2 Akor. 6:3.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambila kwa pabanja khalani ndi nthawi yoyeseza zimenezi.
Mukacoka panyumba ya munthu wokwiya muyenela kukambilana ndi mnzanu za njila yabwino imene mukanayankhila mwininyumbayo.