LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/12 tsa. 1
  • “Khalani Mwamtendele ndi Anthu Onse”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Khalani Mwamtendele ndi Anthu Onse”
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Mwininyumba Wokwiya
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Muzionetsa Khalidwe Lopambana mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 12/12 tsa. 1

“Khalani Mwamtendele ndi Anthu Onse”

1. Ndi uphungu uti wa m’Baibo umene tiyenela kutsatila tikakumana ndi eni nyumba okwiya?

1 Anthu a Yehova amakonda mtendele, ndipo utumiki wathu ndi wamtendele. (Yes. 52:7) Koma nthawi zina timakumana ndi anthu amene amakwiya cifukwa cowafikila pa khomo pao. N’ciani cingatithandize kukhalabe amtendele tikakumana ndi anthu aconco?—Aroma 12:18.

2. N’cifukwa ciani kukhala ozindikila n’kofunika?

2 Khalani Ozindikila: Ngakhale kuti ena amayankha mwaukali cifukwa cotsutsa coonadi, ena angakwiye pa zifukwa zina osati cifukwa ca ulaliki wathu. Mwina angakwiye cifukwa cakuti tafika panthawi yolakwika. Ndipo mwina angakwiye cifukwa ca mavuto amene ali nao. Ndipo ngakhale ngati akwiya cifukwa ca uthenga wabwino, tisaiŵale kuti mwina ayankha conco cifukwa cakuti anauzidwa zabodza. (2 Akor. 4:4) Kukhala ozindikila kudzatithandiza kukhala odekha podziŵa kuti sanakwiyile ife.—Miy. 19:11.

3. Kodi tingaonetse bwanji ulemu kwa mwininyumba?

3 Khalani Aulemu: Anthu ambili m’magawo athu ali ndi zikhulupililo zozika mizu kwambili. (2 Akor. 10:4) Ali ndi ufulu wosankha kumvela kapena iyai. Tisayese kudelela zimene mwininyumba amakhulupilila ndi kuonetsa ngati kuti ife timam’posa. Akatiuza kuti ticoke, ndi bwino kucoka mwaulemu.

4. Kodi kulankhula mwacisomo kumatanthauzanji?

4 Mau Anu Azikhala Acisomo: Ngakhale atinyoze, tiyenela kuyankha mwaulemu ndi mwacisomo. (Akol. 4:6; 1 Pet. 2:23) M’malo mokangana naye, tiyese kupeza mfundo imene tingagwilizane naye. Nthawi zina tingafunse mwininyumba mokoma mtima cifukwa cake akukana. Koma kuti tisaonjezele mkwiyo, ndi bwino nthawi zina kusapitiliza makambilano.—Miy. 9:7; 17:14.

5. Kodi kukhala amtendele mu ulaliki kumabweletsa mapindu otani?

5 Ngati ndife amtendele, mwininyumba angakumbukile kukoma mtima kwathu, ndipo ulendo wina akhoza kumvetsela ngati wina abwelanso kudzamulalikila. (Aroma 12:20, 21) Ngakhale ngati aoneka kuti safuna ngakhale pang’ono, tsiku lina akhoza kukhala m’bale wathu. (Agal. 1:13, 14) Kaya adzalandila coonadi kapena iyai, ife tidzapitiliza kulemekeza Yehova ndi kukometsela ciphunzitso cathu ngati tipitiliza kukhala odziletsa ndi amtendele.—2 Akor. 6:3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani