Potsatila malangizo amene komiti ya utumiki ya mpingo ingapeleke, matebulo ndi mashelufu a mawilo akhoza kuikidwa pa malo amene pamapita anthu ambili m’gawo la mpingo wanu.
Mungacite bwino kuika shelufu kapena thebulo la zofalitsa pa malo amodzi, masiku amodzimodzi ndi nthawi imodzimodzi mlungu uliwonse. Kucita zimenezi kumakhala ndi zotulukapo zabwino, cifukwa anthu amazoloŵela kuona zofalitsa pa mashelufu ndipo amakhala omasuka kufunsa mafunso kapena kutenga zofalitsa.
Yesetsani kukhala womasuka ndi waubwezi. Muzimwetulila. Ngati munthu wacita cidwi ndi zofalitsa zimene zili pa shelufu, wofalitsa mmodzi angayambe kukambilana naye mwina mwa kunena kuti, “Kodi munaganizilapo zimene Baibulo limakamba pa nkhani imeneyi?” Wofalitsa mmodzi kapena aŵili akhoza kukhala pafupi ndi shelufu kapena thebulo la zofalitsa akumacita ulaliki wamwai.
Mungapemphe adilesi ya anthu acidwi. Gwilitsilani nchito fomu ya S-43 kuti mutsimikizile kuti munthu wacidwi afikilidwe.
Njila ya ulaliki imeneyi yakhala ndi zotsatilapo zosangalatsa. Banja lina limene linacokela ku Croatia linafika pa sitolo lina lalikulu ku Lusaka, ndipo litaona zofalitsa zooneka bwino pa shelufu ya mawilo linapempha kuti lijambule shelufu ya zofalitsalo. “Iwo anafuna kudziŵa nkhani zimene zinali m’zofalitsa zathu,” anatelo Haggai amene anali kusamalila shelufu ya zofalitsa pa tsikulo. Iye anaonjezela kuti, “Popeza kuti banjalo silinali kulankhula bwinobwino cingelezi, tinagwilitsila nchito kabuku kakuti, Good News for All Nations. Iwo ananena kuti anakumanapo ndi Mboni za Yehova ku Croatia. Tinawaonetsa webusaiti yathu ndipo tinawapatsa buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Banjalo linakondwela kwambili. Tinapatsana maadilesi ndipo tinawalimbikitsa kuti akaonane ndi Mboni za Yehova akadzabwelela ku Ulaya.”