Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila m’Gawo la Malonda
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Popeza kuti anthu amagwila nchito kwa maola ambili, tingacite bwino kulalikila ku malo amene io amaseŵenzela kuti uthenga wabwino wa Ufumu uwafike. Kulalikila ku malo a malonda kumakondweletsa ndipo kumabala zipatso, cifukwa anthu ambili amapezeka kunchito ndipo anchito amalankhula bwino ndi makasitomala. Kuti ulaliki ukhale wogwila mtima, ofalitsa ayenela kukhala ndi luso la kuzindikila ndipo afunika kuvala ndi kudzikongoletsa moyenela. (2 Akor. 6:3) Conco, woyang’anila nchito ayenela kuona mmene ulaliki ukucitikila m’gawo la malonda, ndi kudziŵa ofalitsa amene akulalikilamo.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pa Kulambila kwanu kwa Pabanja, yesezani ulaliki wacitsanzo umene mufuna kudzagwilitsila nchito mukamalalikila m’gawo la malonda.