Ndandanda ya Mlungu wa September 21
MLUNGU WA SEPTEMBER 21
Nyimbo 53 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 15 ndime 20-23 ndi bokosi pa tsa. 157 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mafumu 19-22 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Mafumu 20:12-21 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Ehudi—Mutu: Yehova Amapulumutsa Anthu Ake (w04 3/15 tsa. 29-31) (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mau Akuti “Ame” Amatanthauza Ciani? (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino.”—Machitidwe 20:24.
Nyimbo 97
Mph. 10: Kodi Tinacita Zotani Caka Catha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Fotokozani zimene mpingo unacita caka catha. Chulani zinthu zabwino zimene mpingo unacita ndipo uyamikileni pa zimenezo. Fotokozani mfundo imodzi kapena ziŵili zimene mpingo uyenela kuongolela caka cino ndipo fotokozani mmene ungacitile zimenezo.
Mph. 10: Kucitila Umboni Mokwanila Kumabala Zipatso. Kukambilana kozikidwa pa Buku Lapacaka la 2015, tsa. 54, ndime 1; tsa. 56, ndime 2, mpaka tsa. 57, ndime 1; ndi tsa. 63, ndime 2 mpaka 64, ndime 1. Mukakambilana citsanzo ciliconse, pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzilapo.
Mph. 10: “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 81 ndi Pemphelo